Chuma mzikho zadothi

Chikhalidwe Komanso Tanthauzo la Mgonero


Listen Later

Chikhalidwe komanso Tanthauzo la Mgonero wa Ambuye

Tikumbukile nthawi imene timakamba za masakalamenti pamene tidanena kuti alipo awiri: ubatizo komanso mgonero wa Ambuye.

Masakalamenti amenewa adakhazikitsidwa ndi cholinga choti aonetsele poyera chikhulupiliro chathu cha uthenga wabwino. Pamene tikondwelera mu mgonero wa Ambuye komanso kutenga mbali pa ubatizo, zonsezi zimatipatsa mwayi oti tionetsele chikhulupiliro chathu poyera.

Anthu atatipeza natifusa kuti kodi ndi chifukwa chiyani mukuchita izi. Yankho lake ndi lakuti, chifukwa cha chimene Yesu Khristu ali komanso zimene adachita. St. Augustine pokamba za masakalamenti adanena kuti: “zizindikilo zakunja komanso zooneka ndi maso za chisomo chauzimu cha mkati mwa munthu.”

Kutanthauza kunena kuti, mbali zonse ma sakalamenti amakhala chizindikilo chimene chimalozela ku chinthu china chosiyana komanso chofunikila kuposa ilo.

Ndingoyelekeza motele, patha kukhala chikwangwani pa msewu chopita ku Lilongwe. Mutha kuchidziwa chikwangwanicho. Mwina mudayimako pafupi ndi chikwangwanicho. Mwinanso mudalozelako anthu ena chikwangwanicho. Ndipo chikwangwanicho mutha kuchidziwa kwambiri ngakhale simudafike malo amene chikulozela. Mukudziwa kuti pali malo otchedwa Lilongwe chifukwa cha chikwangwani. Ndizotheka kuti kuli anthu kumeneko koma simukudziwa chifukwa choti simudapiteko. Pamenepa titha kuona kuti pali kuthekela kodziwa chikwangwani kapena chizindikilo cholozela kanthu kamene inu simudakaone.

Ndi chimodzimodzinso mgonero wa Ambuye. Ndi zotheka ngakhale chimakhala chinthu chovetsa chisoni, koma ndi zotheka kutenga nawo mbali kudya mgonero koma osazindikila chimene umayimila kapena kutionetsela. Ndi chifukwa chake ndi chinthu chofunikila ngati anthu patokha komanso m’mipingo mwathumu kuti tikhale chidwi ndi zinthu zimenezi.

Chimene tikuchiona mu Chipangano Chatsopano chokhudzana ndi ubatizo komanso mgonero ndi chakuti, miyambo imeneyi siyidabwele chifukwa choti anthu adakhala pamodzi nkuyamba kulingalira za mwambo kapena ka bungwe, koma chimene tikuona ndi chakuti zidakhazikitsidwa ndi Mulungu.

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika