Ngati munthu adza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale ake, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga. Ndipo amene ali yense sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga. Pakuti ndani wa inu amene akufuna kumanga nsanja yayitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, awone ngati ali nazo zakuyimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya maziko ake, wosakhoza kuyimaliza, anthu onse woyang’ana adzayamba kumseka iye. Ndikunena kuti, Munthu uyu adayamba kumanga, koma sadathe kumaliza. Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu imzake, siyiyamba yakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikari ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikari zikwi makumi awiri? Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere. Chomwecho ndinena kwa inu, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga.