Chuma mzikho zadothi

Kulungamitsidwa Mutu 2


Listen Later

Monga kwalembedwa, palibe m’modzi wolungama, inde palibe m’modzi; Palibe m’modzi wakudziwitsa, palibe m’modzi wakufunafuna Mulungu; Onsewa apatuka njira, wonsewa pamodzi akhala wopanda phindu; palibe m’modzi wochita zabwino, inde, palibe m’modzi ndithu. M’mero mwawo muli manda apululu; Ndi lilime lawo amanyenga; ululu wa njoka uli pansi pa milomo yawo; M’kamwa mwawo mudzala ndi zotemberera ndi zowawa; Miyendo yawo ichita liwiro kukhetsa mwazi; Kusakaza ndi kusawuka kuli m’njira zawo; Ndipo njira ya mtendere sadayidziwa; Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pawo. Ndipo tidziwa kuti zinthu zili zonse chizinena chilamulo zichiyankhulira iwo ali pansi pa chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi likatsutsidwe pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.

(Rom 3:10-20)

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika