Makolo a Yesu Khristu Monga mwa Thupi
1Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:
2Abrahamu anabereka Isake,
Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.
3Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara.
Perezi anabereka Hezironi,
Hezironi anabereka Aramu.
4Aramu anabereka Aminadabu,
Aminadabu anabereka Naasoni,
Naasoni anabereka Salimoni.
5Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe,
Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute,
6Yese anabereka Mfumu Davide.
Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya.
7Solomoni anabereka Rehabiamu,
Rehabiamu anabereka Abiya,
8Asa anabereka Yehosafati,
Yehosafati anabereka Yoramu,
Ahazi anabereka Hezekiya.
10Hezekiya anabereka Manase,
11Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni.
12Ali ku ukapolo ku Babuloni,
Yekoniya anabereka Salatieli,
Salatieli anabereka Zerubabeli.
13Zerubabeli anabereka Abiudi,
Abiudi anabereka Eliakimu,
Eliakimu anabereka Azoro.
14Azoro anabereka Zadoki,
15Eliudi anabereka Eliezara,
Eliezara anabereka Matani,
16Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu.
17Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.