Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m’masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum’mawa anafika ku Yerusalemu, Nanena, Ali kuti amene adabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tidawona nyenyezi yake kum’mawa, ndipo tidabwera kudzamlambira Iye. Pamene Herode mfumuyo adamva ichi adavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye. Ndipo pamene adasonkhanitsa ansembe akulu onse ndi alembi a anthu, adafunsira iwo, adzabadwira kuti Khristuyo? Ndipo adamuwuza iye, M’Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kudalembedwa kotere ndi m’neneri kuti, Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wam’ng’onong’ono mwa akulu a Yudeya; pakuti wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisrayeli. Pomwepo Herode adawayitana Anzeruwo m’seri, nafunsitsa iwo nthawi yake idawoneka nyenyeziyo. Ndipo adawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mawu, kuti inenso ndidzadze kumlambira Iye. Ndipo iwo, m’mene adamva mfumu, adamuka; ndipo onani, nyenyezi ija adayiwona kum’mawa, idawatsogolera iwokufikira idadza niyima pamwamba pomwe padali kamwanako. Pamene adayiwona nyenyeziyo, adakondwera ndi kukondwa kwakukulu. Ndipo pamene adafika ku nyumba adawona kamwanako ndi Mariya amake, ndipo adagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chawo, nampatsa Iye mphatso zawo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure. Ndipo iwo, pochenjezedwa ndi Mulungu m’kulota kuti asabwerere kwa Herode, adachoka kupita ku dziko lawo panjira yina. Ndipo pamene iwo adachoka, onani, m’ngelo wa Ambuye adawonekera kwa Yosefe m’kulota, nati Tawuka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Aigupto, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuwuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukawononga iko. Ndipo iye adanyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Aigupto. Ndipo adakhalabe kumeneko kufikira adamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa m’neneri kuti, ndidayitana Mwana wanga atuluke mu Aigupto. Pamenepo Herode, powona kuti adampusitsa Anzeruwo, adapsa mtima ndithu natumiza ena kukawononga tiana ta m’Betelehemu ndi ta m’milaga yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating’ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye adafunsitsa kwa Anzeruwo. Pomwepo chidachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya m’neneri, kuti, Mawu adamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo. Koma pamene Herode adamwalira, onani, m’ngelo wa Ambuye adawonekera m’kulota kwa Yosefe mu Aigupto. Nanena, Tawuka, nutenge kamwana ndi amake nupite kudziko la Israyeli; chifukwa adafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako. Ndipo iye adawuka natenga kamwana ndi amake, nalowa m’dziko la Israyeli. Koma pamene iye adamva kuti Arikelao adali mfumu ya Yudeya m’malo mwa atate wake Herode, adachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene adachenjezedwa ndi Mulungu m’kulota, adapita nalowa ku mdera lina la Galileya: Ndipo adadza nakhazikika mumzinda wotchedwa Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.