Sign up to save your podcasts
Or

Ambuye wathu Yesu Khristu anabadwa modabwitsa. Luka 2:1-7
Ndipo kudali masiku aja, kuti lamulo lidatuluka kwa Kayisala Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe. Ndiko kulembera koyamba pokhala Kureniyo kazembe wa Suriya. Ndipo onse adapita kukalembedwa, munthu aliyense ku mzinda wake. Ndipo Yosefe yemwe adakwera kuchokera ku Galileya, ku mzinda wa Nazarete, kupita ku Yudeya, ku mzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, (chifukwa iye adali wa banja ndi fuko lake la Davide:) Kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Mariya, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu adali ndi pakati. Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala adakwanira kuti abeleke. Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namukulunga Iye mu nsalu, namgoneka modyera ng’ombe, chifukwa kuti adasowa malo m’nyumba ya alendo.
(Luk 2:1-7)
By John Joseph MatandikaAmbuye wathu Yesu Khristu anabadwa modabwitsa. Luka 2:1-7