Chuma mzikho zadothi

Kufunikila kwa Imfa ya Ambuye Yesu


Listen Later

Koma atafika Khristu, Mkulu wansembe wa zabwino ziri mkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi; Kosati mwa mwazi wa mbuzi ndi ana ang’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, adalowa kamodzi kumalo wopatulika, atalandirapo chiwombolo chosatha chifukwa cha ife. Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, ndi makala ang’ombe yamthandi wowazawaza pa iwo wodetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi: Koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene adadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo? Ndipo mwa ichi Iye ali nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti popeza kudachitika imfa yakuwombola zolakwa za pa chipangano choyamba kuti iwo, woyitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha. Pakuti pamene pali pangano pafunika pafike imfa ya mwini panganolo. Pakuti chipangano chikhala ndi mphamvu atafa mwini wake; pakuti sichikhala ndi mphamvu konse pokhala mwini pangano ali ndi moyo; Momwemonso chipangano choyambacho sichidakonzeka chopanda mwazi. Pakuti pamene Mose adayankhulira anthu onse lamulo liri lonse monga mwa chilamulo, adatenga mwazi wa ana a ng’ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiyira ndi hisope, nawaza buku, ndi anthu onse, Nati, Uwu ndi mwazi wa chipangano Mulungu adakulamulirani. Ndiponso chihema ndi zotengera zonse za utumikiro adaziwaza momwemo ndi mwaziwo. Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang’ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo popanda kukhetsa mwazi palibe kumasuka. 

(Heb 9:11-22)



...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika