
Sign up to save your podcasts
Or


Tsoka kwa inu, pamene anthu adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo awo adawatero momwemo aneneri wonama. Koma ndinena kwa inu akumva, kondanani nawo adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu. Dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe. Ndipo kwa Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso limzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya akonso. Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso. Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitireni inu, muwachitire iwo motero inu momwemo. Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti wochimwa womwe akonda iwo akukondana nawo. Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu wochimwa amachitanso chomwecho. Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti onse anthu wochimwa amakongoletsa kwa wochimwa amzawo, kuti alandirenso momwemo. Koma kondanani nawo adani anu, ndikuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekezera kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yayikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma osayamika ndi woyipa. Khalani inu a chifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musaweruze ndipo simudzaweruzidwa, musawatsutse ndipo simudzatsutsidwa, khululukirani ndipo mudzakhululukidwa. Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani pa chifuwa chanu, pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu.
(Luk 6:26-38)
By John Joseph MatandikaTsoka kwa inu, pamene anthu adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo awo adawatero momwemo aneneri wonama. Koma ndinena kwa inu akumva, kondanani nawo adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu. Dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe. Ndipo kwa Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso limzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya akonso. Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso. Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitireni inu, muwachitire iwo motero inu momwemo. Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti wochimwa womwe akonda iwo akukondana nawo. Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu wochimwa amachitanso chomwecho. Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti onse anthu wochimwa amakongoletsa kwa wochimwa amzawo, kuti alandirenso momwemo. Koma kondanani nawo adani anu, ndikuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekezera kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yayikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma osayamika ndi woyipa. Khalani inu a chifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musaweruze ndipo simudzaweruzidwa, musawatsutse ndipo simudzatsutsidwa, khululukirani ndipo mudzakhululukidwa. Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani pa chifuwa chanu, pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu.
(Luk 6:26-38)