Chuma mzikho zadothi

Mtanda Odabwitsa


Listen Later

Ndipo pomwepo m`mawa adakhala upo ansembe akulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato. Ndipo Pilato adamfunsa Iye, Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda? Ndipo poyankha adati kwa iye, Mwatero ndinu. Ndipo ansembe akulu adamnenera Iye zinthu zambiri koma sadayakhe kanthu. Ndipo Pilato adamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Tawona, akuchitira umboni Iwe mokutsutsa zinthu zambiri zotere. Koma Yesu sadayankhenso kanthu; kotero Pilato adazizwa. Tsopano amkawamasulira paphwando wa mndende m’modzi, amene iwo adamfuna. Ndipo adalipo wina dzina lake Baraba, womangidwa pamodzi ndi ena wopanduka, amene adapha munthu mumpanduko. Ndipo khamu lidafuwuula niliyamba kupempha Iye  kuti achite monga adali kuwachitira iwo. Koma Pilato adawayankha iwo, nanena Kodi mufuna ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda? Pakuti adazindikira kuti ansembe akulu adampereka Iye mwa njiru. Koma ansembe akulu adasonkhezera anthu, kuti makamaka awamasulire Baraba. Ndipo Pilato adayankha natinso kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula Mfumu ya Ayuda? Ndipo adafuwulanso, Mpachikeni Iye. Pamenepo Pilato adanena nawo, Chifukwa chiyani, Iye adachita choyipa chotani? Koma iwo adafuwulitsatu, Mpachikeni Iyeyo. Ndipo Pilato pofuna kuwakhazikitsa mtima anthuwo, adawamasulira Baraba, nampereka Yesu, atamkwapula kuti akapachikidwe. 

(Mar 15:1-15)

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika