LERO TIKUFUNA TIONE KUTI KODI NDI CHIFUKWA CHIYANI MPINGO UMAKUMANA PAMODZI.
Pali zinthu zambiri zimene titha kunena zokhudzana ndi chifukwa chimene mpingo umakumanila pamodzi – kupemphera, kukhala pa chiyanjano, kuphuzitsidwa, kupembedza Mulungu, ndi zina.
Lero tikhazikika pa ndime imene imatiuza chifukwa chimodzi chimene chimapangitsa mpingo kuti uzikumana pamodzi komanso tiona chifukwa chimene kukumana kumeneku ndi ntchito yofunikila kwambiri pa mpingo.
TIYENI TIWERENGE AHEBERI 10:19-25
“Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.”
Monga mwa ndime imeneyi, tiyeni tigawane zimene tikuphuzila mu fundo ziwiri:
Fundo yoyamba, patokha timagwedezeka m’chikhulupiliro chathu.
Ndime imeneyi ikutilimbikitsa kuti “tigwiritse chibvomerezo cha chiyembekezo chathu osagwedezeka.” Kutanthauza kunena kuti sititalikilana kugwedezeka pa chikhulupiliro chathu, ndipo tikuyenela kukumbutsidwa kuti tigwilitsitse. Pamene tasiya kusonkhana pamodzi, timataya chilimbikitso chotele kuchokela kwa anzathu.
Tiyeni tione zimene zikuchitika pa ndime imeneyi polingalira buku lonse la Aheberi. Mu buku lonseli la Aheberi, tikupatsidwa machenjezo osiyanasiyana zokhudzana ndi tchimo ndi kubwelera m’mbuyo.
Tiyeni tiwerenge Aheberi 3:12-13
“Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo. Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.”
Ndime imeneyi ikutichenjeza za mtima osakhulupilira. Tikuyenela tikhale chidwi kuti mitima yathu isaumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.
Ndiye mawu oti “chinyengo cha tchimo” akutanthauzanji? Tchimo mwa chikhalidwe chake limatha kutinyenga. Limatipusitsa, ndipo sitidziwa kuti tapusitsidwa. Zimene zimapangitsa kuti chikhale chinthu choopsya kwambiri.
Tiyeni tingoganizila m’mene zimaonekela kuti munthu wanamizidwa ndi tchimo. Munthu ali pabanja bwinobwino koma chifukwa chonamizidwa ndi tchimo amayamba kuona akazi ake kapena amuna ake kuti ndi osakwanila. Zotsatila zake amayamba kuyenda njira za mseli ndi akazi ena kapena amuna ena nkumaona ngati ndilo yankho loyenelera. Pamenepa ndiye kuti tchimo lamupusitsa munthu ameneyu.
Ndiye tikaona pa ndime imeneyi, ikutiphuzitsa kuti tizilimbikitsana wina ndi mnzake pafupipafupi ndi cholinga choti tipewe kuumitsidwa mtima ndi chinyengo cha tchimo. Ngati ndanyengedwa ineyo, ndikusowekela munthu wina kuti andithandize ndidziwe pamene ndanyengedwapo chifukwa choti sindingathe kuona kuti ndanyengedwa. Ndikusowekela choonadi komanso maganizidwe ena kuchokela kwa anthu ena kundikumbutsa choonadi cha Mulungu.
Patokha, timagwedezeka m’chikhulupiliro chathu, mitima yathu imaumitsidwa, ndipo timanyengedwa ndi tchimo lathu. Ndi chifukwa chake tikuyenela kumakumana pamodzi ndi azathu kuti tipeze thandizo kuchokela kwa azathuwo.