Sign up to save your podcasts
Or

Tsopano tafika gawo lathu lomaliza. Ndikhulupilira kuti pofika pano muli ndi chidziwitso chozama komanso kuvetsetsa kwabwino pa zimene Mawu a Mulungu ali. Mu njira ina, kuvetsetsa kwabwino kumeneku kwa Mawu a Mulungu kutha kutifoketsanso. Kutanthauza kuti, tavetsa bwino za kuzama kwa Baibulo komanso m’mene anthu ophuzila akangalika m’moyo wawo kulisanthula; pa chifukwa ichi, kuwerenga Baibulo itha kuoneka ntchito yovuta zedi. Lero tikufuna tione pamene tingayambile.
Tiyambe ndi nkhani yapemphero
Ndiye ndineneletu kuti sititenga nthawi yaitali kukamba nkhani ya pemphero, chifukwa phuzilo lathu la 7 tidakamba kale zambiri zambiri. Tidaona kunena kuti tipemphere kuti tikhale ndi mtima wodzichepetsa, kuti tigonjele Mawu a Mulungu. Komanso tidaona kuti tipemphelere kuti Mulungu atiteteze, atitsogolere, atipatse nzeru, atithanzize, komanso aonetsele ulemelero wake.
Ø Koma ngakhale sititenga nthawi yaitali kukamba za pemphero, tikuyenela kukumbuka kuti pemphero likuyenela lisasowekele pamene tikuwerenga Baibulo. Ndi lofunikila kwambiri.
Ø Pempherani musadayambe kuwerenga Baibulo, “Mulungu, chonde tsekulani maso anga.” Pempherani pamene mukuwerenga kuti maganizo anu akhazikike komanso muvetsetse, “Mulungu, ndithandizeni kuti ndikhazikike ndi kuvetsa mawu anu.” Pempherani mukamaliza, “Mulungu, ndithandizeni kuti ndiyende ndi kugwilitsa ntchito Mawu anu m’moyo wanga.”
Ø Mulungu alibe malire. Inu ndi ine tili ndi malire. Tikusowekela thandizo lake.
By John Joseph MatandikaTsopano tafika gawo lathu lomaliza. Ndikhulupilira kuti pofika pano muli ndi chidziwitso chozama komanso kuvetsetsa kwabwino pa zimene Mawu a Mulungu ali. Mu njira ina, kuvetsetsa kwabwino kumeneku kwa Mawu a Mulungu kutha kutifoketsanso. Kutanthauza kuti, tavetsa bwino za kuzama kwa Baibulo komanso m’mene anthu ophuzila akangalika m’moyo wawo kulisanthula; pa chifukwa ichi, kuwerenga Baibulo itha kuoneka ntchito yovuta zedi. Lero tikufuna tione pamene tingayambile.