Chuma mzikho zadothi

Kodi mpingo ndi chani?


Listen Later

Sabata ino tikuyamba kuona zokhudzana ndi mpingo

Palibe chinthu chopambana kuposa kukhala pa mpingo. Mpingo ngati banja la ana a Mulungu, limakhala ndi udindo waukulu pa wina ndi mnzake.

Alipo anthu ena lero amene sazindikila bwinobwino udindo wa mpingo pa moyo wawo. Amaona ngati kulumikizana ndi Mulungu pawokha ndi bwino kusiyana ndi kukhazikika pa mpingo. Mwina kumayika patsogolo zinthu ngati mpira, kugona kapena maphuzilo pamwamba pa mpingo. Kuonjezela pamenepo, nthawi zina kumapezeka kuti timautumiki tina tikufuna kukhala pamwamba pa mpingo mpaka kupangila ma membala atchalitchi kumadzipeleka kwakukulu ku utumiki uja kusiyana ndi ku mpingo kwawo.

Pamene tikuyamba gawo ili, ndikuyembekezela kuti mukhala ndi mwayi ovetsetsa kuti kodi mpingo ndi chani, m’mene umayendela, koma kufunikila kwake m’moyo mwathu. Mulungu adayika mpingo kuti ukhale chilimbikitso kwa ife komanso kuti tikule limodzi mwa Khristu, anthu ena ndi kumayang’anila moyo wanu wa uzimu, kumva uthenga wabwino kulalikidwa, kukondwela ndi anthu osiyanasiyana, kuyenda limodzi m’moyo komanso kudutsa mzowawa pamodzi. Mpingo ndi chinthu chimene Mulungu adapeleka mwa chisomo komanso chikondi chake kwa anthu ake.

Tikawelenga Machitidwe 9, Saulo akuzuza mpingo, ndipo Yesu akumufusa kuti, “Saulo, Saulo, ndi chifukwa chiyani ukundizuza ine?” kuonetsela kuti chimene tikuchitila mpingo ndi chimene tikuchitila Khristu. Tikuyenela tikonde mpingo ngati timakonda Yesu. Pemphero langa ndi lakuti pamene tizidzamaliza chiphuzitso ichi tidzazidwa ndi nzeru komanso chikondi pa mpingo wake wa Mulungu, ndi kubweletsa ulemelero wochuluka kwa Yesu. Tikule m’chikondi chathu cha pa mpingo pamene tikukula m’chikondi chake pa Yesu, amene adatikonda poyamba.

Lero tiyambe ndi funso lakuti, kodi mpingo ndi chani?

Mawu amene amatanthauzidwa “mpingo” m’Baibulo akuchokela ku mawu ena a chiGreek amene amatanthauza “msonkhano” kapena “nkumano.”

Nthawi zina timagwilitsa ntchito mawu oti “mpingo” kuyimila mpingo onse wa dziko lapansi – amene ndi anthu onse a Mulungu pa dziko lonse lapansi. Nthawi zinanso timagwilitsa ntchito mawu oti “mpingo” kuyimila anthu osonkhana pa dela, kusonkhana ndi okhulupilira ena.

Mwina mudavako kuti mpingo si nyumba yopempheleramo. Mpingo ndi anthu. Ndiye anthu amene ndi mamembala a kudela kwanuko ndiwo mpingo wanu. Ndiye mpingo wakudela uli gawo la mpingo onse wa okhulupilira pa dziko lonse lapansi.

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika