Chuma mzikho zadothi

Chikhalidwe Komanso Tanthauzo la Ubatizo


Listen Later

Tipite ku nkhani ya lero: chikhalidwe komanso tanthauzo la ubatizo.

Tikuyenela tizindikile kuti nkhani ya ubatizo ndi nkhani imene yabweletsa mpungwepungwe pakati pa mipingo. Ndipo pena zimakhala zovetsa chisoni kuti akhristu amapezeka kuti akugawanikana pa nkhani imeneyi. Kusiyana kwathu pa nkhani ya ubatizo kusatisokoneze mu njira ina iliyonse. Chofunikila ndi kuonetsetsa kuti pa ziphuzitso zikuluzikulu za Baibulo komanso uthenga wabwino ndife ogwilizana. Nkhani ya tanthauzo komanso kachitidwe ka ubatizo kasakhale patsogolo ngati nkhani ya chipulumutso. Ikhale nkhani yobwela pambuyo.

Pokhapokhapo pamene gulu lina la anthu litenga ubatizo ngati chipulumutso, tikuyenela kukanitsitsa ndi cholinga choti chipulumutso cha Ambuye wathu Yesu Khristu monga mwa Baibulo chisapeputsidwe.

“Ubatizo umaonetsela umodzi wathu ndi Khristu. Ndi ubatizo mu dzina la Khristu, kutifananitsa ndi Khristu komanso kutiphatika mwa iye. Umaonetsela kukhala pamodzi ndi iye ndipo umasindikiza kupezeka naye mu imfa yake, kuyikidwa m’manda kwake komanso kuuka kwake. Umachitila umboni komanso kuonetsela umodzi wa pangano ndi umodzi mwa uzimu ndi Ambuye Yesu amene adauka kwa akufa. Timakhala ndi Khristu. Tamangililidwa mwa Khristu. Tazikidwa mwa Khristu. Tigawana naye mu chimene ali komanso zopindula zake. Tikondweletsedwa ndi cholowa chake. Tili ndi maufulu ake.” Donald Macleod.

Koma funso limene limavuta kwambiri ndi lakuti, Kodi makolo okhulupilira ali ndi ufulu kuti aonetsele chikhulupiliro chawo pa ubatizo wawo pamodzi ndi apabanja awo? Kodi amene ayenela kubatizidwa likhale kholo lokhalo limene lakhulupilira kapena ndi banja lake lonse? Kuti tiyankhe bwino funso limeneli tikuyenela tione zimene zinali kuchitika mu chipangano chatsopano.

Pamenepa titha kuona kuti zikuyenela kutelo. Tikumbukilenso kunena kuti pamene Mulungu adakhazikitsa pangano lake ndi Abraham, adanenetsa kuti chizindikilo cha pangano la uzimu chikuyenela kupelekedwa kwa ana awo. Momwemonso ubatizo ukuyenela kufikila ana a makolo okhulupilira.

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika