Sign up to save your podcasts
Or

Ndiye tiyeni tifike pa funso lakuti: kodi Baibulo timawerenga motani? Litha kuoneka ngati funso lodabwitsa kwambiri popeza ambiri mwina timadziwa kuwerenga Baibulo. Koma chimene tikufuna tione ndi chakuti, Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena onse amene adalembedwa, ndi chifukwa chake akhristu akuyenela kufikila kuwerenga Malemba Opatulika mosiyanitsa ndi mabuku ena.
Chinthu choyamba chimene tikufuna tichione ndi chakuti, tikuyenela tiwerenge Baibulo mwauzimu.
Ahebri 4:12-13 akunena kuti: “Pakuti mawu a Mulungu ali a moyo, ndi wochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima. Ndipo palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pake pa Iye amene tikuyenela kufotokozela.”
Ø Ndiye chinthu chimodzi chimene tikuphuzila pa ndime imeneyi ndi chakuti Mawu a Mulungu ndi amoyo. Mawu amaonetseladi kuti ndi amoyo ndipo ali ndi kuthekela kuweruza mtima wanu komanso kukubweletsani poyera.
Ø Kachiwiri, popeza kuti buku ndi la moyo ndipo timakhulupilira moona mtima kuti umu ndi m’mene Mulungu amalankhulira nafe, tikuyenela kulifikila mwa ulemu onse.
Ø Pali njira zambiri zimene tingathe kufikila mwaulemu, koma njira yoyambilira ndi kufikilako mwakupemphela.
Ø Kumbukilani zinthu zitatu zimene tidaona zokhudzana ndi Malemba Opatulika pa phuzilo lachiwiri lija: kuti Baibulo lidauzilidwa, lilibe cholakwa ndipo lilibe chophonyetsa china chilichonse. Komanso tidaona kuno ndi lopanda malire.
Ø Tiyeni tiwerenge Yesaya 40:6-8: “Mawu a wina ati, ‘Fuula!’ Ndipo ndinati, ‘Kodi ndifuule chiyani?’ Thupi lonse ndi udzu, kukongola kwake kuli ngati duwa la m’thengo. Udzulu uwuma, duwa lifota pamene mpweya wa Yehova uliuzila; zoonadi anthu ndi udzu. Udzu uwuma, duwa lifota, koma mawu a Mulungu wathu adzayima kwamuyaya.”
Ø “…mawu a Mulungu wathu adzayima kwamuyaya.”
By John Joseph MatandikaNdiye tiyeni tifike pa funso lakuti: kodi Baibulo timawerenga motani? Litha kuoneka ngati funso lodabwitsa kwambiri popeza ambiri mwina timadziwa kuwerenga Baibulo. Koma chimene tikufuna tione ndi chakuti, Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena onse amene adalembedwa, ndi chifukwa chake akhristu akuyenela kufikila kuwerenga Malemba Opatulika mosiyanitsa ndi mabuku ena.