Chuma mzikho zadothi

Kodi Baibulo timawerenga motani? Gawo 2


Listen Later

Chinthu choyamba chimene tikufuna tikhazikikepo ndi nkhani ya dongosolo la magawidwe ake.

Tidaona kale kuti Baibulo ndi nkhani imodzi imene yagawidwa mzipangano ziwiri.

Ø Chipangano Chakale – chimene chili ndi magawo ake asanu akuluakulu ndipo magawo ake ndi awa: Mbiri, Chilamulo, Ndakatulo, Nzeru, komanso Aneneri (Akulu komanso Ang’ono).

Ø Ndiye pali Chipangano Chatsopano – chimene chili ndi magawo ake anayi akuluakulu omwe ndi: Uthenga Wabwino, Mbiri, Makalata, komanso Mavumbulutso a Chimalizilo.

Ø Tsopano chimene tikuyenela kuzindikila ndi chakuti: simungathe kuwerenga mabuku onse a m’Baibulo mofanana. Inde, taona kale kuti tikuyenela kufikila mabuku onse mwakupemphera – modzichepetsa komanso chidziwitso cha ulamuliro wa Malemba Opatulika – koma mabuku amawerengedwa mosiyanasiyana.

Ndiye tiyeni tione kuti zimenezi zikutanthauza chiyani.

Ø Magawo akuluakulu aja ndanena aja titha kunena ndi mitundu ya zolembalemba. Kutanthauza kunena kuti pali mitundu yosiyanasiyana kapena kalembedwe kosiyanasiyana.

Ø Mwa chitsanzo, mtundu wokamba nkhani ukuyenela kuwerengedwa mosiyana ndi mtundu wa ndakatulo. Nkhani ikalembedwa titha kuyimva mosapinda kusiyana ndi ndakatulo.

Ndiye titha kumafusa kuti kodi nanga ndi chifukwa chiyani Mulungu adatipatsa mitundu ya kalembedwe yosiyanasiyana?

Ø Mwachidule titha kuyankha kunena kuti, Malemba Opatulika ali ndi mitundu yosiyanasiyana ndi cholinga choti akuthandizeni inuyo – atithandize tonse. Muli ndi kamvedwe ka zinthu, ndiye pali magawo m’Mawu ake, mwachitsanzo Masalimo, amene amayankhula ndi mtima wanu. Muli ndi maganizo, ndiye pali makalata, monga Aroma, amene amatambasula maganizo anu. Ndiye titha kuona kuti Mulungu amayankhula ku gawo lina lililonse la moyo wanu.

Ø Chimene ndiye chifukwa chimene Mulungu adatipatsila mitundu yosiyanasiyana kuti akhudze magawo onse a moyo wathu. Nthawi zonse tikamawerenga Baibulo tizidzifunsa kuti, kodi ndikuwerenga mtundu wanji? Funsoli ndi lothandiza kuvetsetsa kwathu komanso kukondwelera.

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika