Sign up to save your podcasts
Or

Patokha timalowelera
Galatians 6:1
Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe.
Yakobo 15:19-20
19Abale anga, ngati mmodzi wa inu apatuka pa choonadi ndipo wina wake ndi kumubweza, 20kumbukirani izi: Aliyense wobweza wochimwa kuchoka ku cholakwa chake, adzamupulumutsa ku imfa ndi kukwirira machimo ambiri.
Mpingo Umatibweza
Mateyu 18:15-17
15 “Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo. 16Koma ngati sakumvera, katenge wina mmodzi kapena ena awiri, ‘kuti nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.’ 17Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho.
18 “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba.
Aheberi 12:9-11
9Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo? 10Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima. 11Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.
Luka 15:1-7
1Tsopano amisonkho ndi “ochimwa” ankasonkhana kudzamvera mawu ake. 2Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, “Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo.”
3Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili: 4“Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza? 5Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe 6ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija.’ 7Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”
1 Petro 3:18
18Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.
By John Joseph MatandikaPatokha timalowelera