Chuma mzikho zadothi

Kukhala Membala Pa Mpingo


Listen Later

Lero tikufuna tione za kukhala membala pa mpingo

Chiyambileni kuona za mpingo takhala tikuona za tanthauzo la mpingo komanso m’mene umagwilira ntchito. Koma zimatheka kuti anthu ambiri atha kumapemphela ndi anzawo pa mpingo koma sadutsa njira zimene zimafunikila kuti akhale membala wodziwika pa mpingo.

Zimenezi zikuchulukila kwambiri mu chikhalidwe chathu lero lino. Anthu amene amadzitcha kuti ndi akhristu amatha kuchoka mpingo uwu kupita mpingo wina, kufunafuna zambiri kuti mwina akhale ndi moyo wauzimu opanda vuto. Ena atha kumapita ku tchalitchi koma safuna kukhala membala, bola azingopemphera nawo.

Chimene tikuyenela kuzindikila ndi chakuti, simunganene kuti ndinu chiwalo cha mpingo wa Khristu ngati mulibe malo anu okhazikika opemphelera amene anthu amakudziwani. Ndi zosatheka. Simunganene kuti inuyo ndinu m’Malawi koma ku Malawi kuno kulibe mudzi wanu kapena amfumu okuchitilani umboni kuti ndinu m’Malawi.

Chipangano chatsopano chimayembekezela kuti mkhristu weniweni akhalanso membala wa pa mpingo.

Monga takhala tikuonela, tikuyenela kufufuza zimene Malemba Opatulika akuphuzitsa pa nkhani imeneyi. Kodi Mawu a Mulungu amalamulira kuti tikhale mamembala m’mipingo mwathumo? Kodi nkhani ya umembala pa mpingo ikuchokela mu Baibulo kapena idangochoka m’maganizo mwa anthu? Ngakhale titha kunena kuti palibe vesi imene idzatiuza kuti “ukuyenela kukhala membala wa pa mpingo,” timapeza fundo za umembala mu chipangano chatsopano. Tiyeni tione ndime zingapo.

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika