Chuma mzikho zadothi

Kukondana Wina ndi Mnzake


Listen Later

Mateyu 25:34-40


34 “Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko. 35Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira, 36ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.’

37 “Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa? 38Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani? 39Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?’

40 “Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika