Chuma mzikho zadothi

Kuphuzila kukonda Akhristu azathu


Listen Later

Lero tikupitiliza kulingalira zifukwa zimene tikusowekela kukhala pa mpingo.

Sabata yatha, tidayamba kuyankha funso limeneli pakunena kuti tikusowekela mpingo popeza kuti timayanjanitsidwa ndi okhulupilira ena mwa Khristu komanso popeza timakula pamodzi kufikila kukula mwa Khristu ndi okhulupilira ena. Tikapanda kulabadila mpingo, zili ngati mamuna kusalabadila mkazi wake kapena gawo limodzi la thupi lanu kumakula mosagwilizana ndi thupi lonse. Zotsatila zake zitha kukhala zoyipa kuchitika zinthu zotele.

Lero, tionjezela fundo ina pa yankho lathu, pamene tikufuna kuona kuti tikusowekela mpingo chifukwa cha kuti tikuyenela kuphuzila kukonda iwo amene Yesu amawakonda.

Chimapangitsa ndi chiyani kuti kukonda anthu ena mu mpingo kukhale kovuta?

Anthu atha kutichitila zinthu zosatisangalatsa, kutikhumudwitsa, kukhala ovuta kuwafikila chifukwa cha machitidwe awo, ndi zinthu zina zingapo. Pamene pali kulimbana kapena anthu ndi osiyana ndi ife, zimakhala zinthu zovuta kuti tiwakonde. Koma vuto lalikulu, si anthu ena, koma ifeyo eni ake. Pamene ndi zovuta kuti tikonde anthu ena, tikuyenela tidziyang’ane tokha komanso tchimo ndi kudzikuza kumene kuli mu mtima mwathu. Vuto si lakuti anthu enawo ndi odzikonda kapena ovuta, vuto ndi lakuti ifeyo sitikuonetsa chikondi.

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika