Sign up to save your podcasts
Or

Lero tikufuna tione za kuyanjanitsidwa ndi Khristu komanso kukula pamodzi.
Funso limene tingayambe nalo ndi lakuti; ndi chifukwa chiyani tikusowekela mpingo m’moyo mwathu? Masabata akubwela kutsogolowa tikhala tikuona kuti pali zifukwa zingapo zimene tikusowekela mpingo m’moyo mwathu. Sabata ino, tikhazikika pa zinthu ziwiri pamene tikuyankha funso limeneli. Timasowekela mpingo popeza tayanjanitsidwa ndi Khristu komanso chifukwa choti timakula pamodzi ndi anzathu osati patokha.
Tikaona nkhani ya kuyanjanitsidwa ndi Khristu
Tiwelenge poyamba
Aroma 12:4-5
“4Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana. 5Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake.”
Ndime imeneyi ikukamba za mpingo ngati thupi, fundo imene tidayiona kale m’mbuyomu. Ndiye nkumati akutanthauza chiyani akamati ndife “thupi limodzi mwa Khristu, komanso aliyense payekhapayekha ziwalo za wina ndi mnzake”?
Zimenezi zikutanthauza kuti Khristu wayanjanitsa anthu ake kuti akhale thupi limodzi umene uli mpingo, ndipo pa chifukwa chimenechi iwo ali olumikizika wina ndi mnzake. Sizingatheke kuti Khristu angayanjanitse anthu ake ngati mpingo kenako nkumatiso mpingo ukhale ogawanikana wina ndi mnzake, ayi.
Chimene chikukambidwa pamenepa ndi chakuti, ndife olumikizika wina ndi mnzake komanso tili ndi udindo wina aliyense ndi mnzake. Zimakhala zovetsa chisoni kuona kuti nthawi zina anthu ena amadziona kuti alibe udindo pa mamembala anzawo ngati kuti ali pawokhawokha. Tikuyenela kuzindikila udindo wathu wina ndi mnzake.
Ndife amodzi. Ndife banja limodzi la iwo amene aitanila pa dzina la Khristu.
By John Joseph MatandikaLero tikufuna tione za kuyanjanitsidwa ndi Khristu komanso kukula pamodzi.