Chuma mzikho zadothi

Umunthu wa Yesu Khristu


Listen Later

PACHIYAMBI panali Mawu, ndipo Mawu adali ndi Mulungu, ndipo Mawu adali Mulungu. Awa adali pachiyambi ndi Mulungu. Zinthu zonse zidalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikadalengedwa kanthu kena kali konse kolengedwa. Mwa Iye mudali moyo; ndi moyowu udali kuwunika kwa anthu. Ndipo kuwunikaku kudawala mumdima; ndi mdimawu sudakuzindikira. Kudali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake ndiye Yohane. Iyeyu adadza mwa umboni, kudzachita umboni za kuwunikaku, kuti anthu onse kudzera mwa iye akakhulupirire. Iye sindiye kuwunikaku, koma adatumidwa kukachita umboni wa kuwunikaku. Uku ndiko kuwunika kwenikweni kumene kuwunikira anthu onse akulowa m’dziko lapansi. Adali m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye, koma dziko lapansi silidamzindikira Iye. Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sadamlandira Iye. Koma onse amene adamlandira Iye, kwa iwo adapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; Amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu. Ndipo Mawu adasandulika thupi nakhazikika pakati pa ife, ( ndipo tidawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate), wodzala ndi chisomo ndi chowonadi. Yohane achita umboni za Iye, nafuwula nati, Uyu ndiye amene ndidanena za Iye, wakudzayo pambuyo panga adalipo ndisanabadwe ine; chifukwa adakhala woyamba wa ine. Chifukwa mwa kudzala kwake tilandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo. Chifukwa chilamulo chidapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi chowonadi zinadza mwa Yesu Khristu. Kulibe munthu adawona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pachifuwa cha Atate, Iyeyu adafotokozera. 

(Joh 1:1-18)

...more
View all episodesView all episodes
Download on the App Store

Chuma mzikho zadothiBy John Joseph Matandika