Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Download on the App Store

Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine episodes

  • Mphamvu ndi chisankho cha mulungu/Selection and sovereignty of God

    Luka 1:57-80 ikukamba zokhuza chithu chapadera chokhuza

    mulungu chimene mavesi ena a muchaputa ichi akamba kale. Kufotokozera komwe kwapelekedwa kale kukugwirizana ndi maulosi ena omwe amakamba za kubadwa kwa mesiya. Mulungu amasankha mu mphamvu yake yemwe akufuna kumugwiritsa ntchito pofuna kukwaniritsa zolinga zake. Tsopano kuti timvetse zokhuza mphamvu ndi chisankho cha mulungu, mavesi a 57-80 a Luka akuyankhulapo momveka bwino pa zimenezi. Choyamba,
    mulungu akusankha mtsikana ozichepesa osauka ochokera kumnzinda osaziwika yemwe dzina lake ndi Maria. Ngelo Gabriel ochokera kwa mulungu anapereka uthenga kwa Maria
    kuti azakhala ndi pakati pa mzimu ndipo mwana obadwayo azakhala mwana wa wam’mwamwambayo. Maria anayilandira nkhaniyi ndipo anafuna kuwuza m’bale wake Elizabeti. Koma ngelo uja asanapite anamuuza Maria za m’bale wakeyo kuti anali ndi pakati mu ukalamba wake chifukwa sankabereka. Iye anachita izi kumusimikizira Maria kuti palibe chomukanika mulungu. Chachiwiri, mulungu akukamba momveka bwino malo, nthawi
    komanso motani momwe mwanayo azabadwire. Maulosi amanena kuti mwanayo azabadwira ku mnzinda wa Betelehemu mudzi wa Davide ndipo ndi komwe anabadwira. Mulungu akuwonetsetsa kuti zichitike malingana ndi ulosi wake ndipo zinachitikadi. Izi zimatithandizira kuzindikira kuti mulungu ndi wamphamvu
    zonse ndipo amalamulira zonse zochitika pa dziko lapansi. Tsopano, kudziwa izi zokhuza mulungu, zitanthauzanji kwa ife? Izi zimathandizira ife kudziwa kuti mulungu samasintha. Iye anali mulungu yemweyo munthawi yakale, iye ali mulungu yemweyo
    munthawi yatsopanoyi komanso apitiriza kukhala mulungu yemweyo munthawi yakutsogolo ndipo tikhoza kumudalira chifukwa samakhumudwitsa.

     

    Luke 1:57-80 talks about something special about God that other verses of this chapter have already discussed. The explanation given here agrees perfectly with all the other prophecies foretelling the birth of messiah. God chooses whomever he wants to use in order to fulfill his purposes. Now to understand clearly about selection and sovereignty of God, verses 57-80 of Luke makes a clear comment on that issue. Firstly, God chooses a noble village girl called Mary who is lowly and poor from a small town. Angel Gabriel from God appears to Mary and gives her the news that she will conceive a child with the power of the spirit from God and the child to be born will be called the son of the highest God. Mary accepts the great news and wants her cousin Elizabeth to know. But before the angel goes back to heaven, he tells her about Elizabeth who also has conceived a child in her old age because she was known to be barren. The angel does this to assure her that nothing is impossible to God. Secondly, God makes it clear how, where and when the messiah would be

    born. Prophecies foretell that the child would be born in a small town called Bethlehem, the city of David and that’s exactly where the child is born. This helps us to understand that God is sovereign and that he controls every event that unfolds on earth. Now, knowing that about God, what does it mean to us? This helps us
    to understand that God never changes. He was the same God in the past, he is the same God in the present and he continues to be the same God in the future and we can trust him completely because he never disappoints.  

    39 min
  • Mulungu akonda anthu ake powapatsa mpulumutsi/God gives his people a savior out of love

    Luka 1:39-45 Maria azonda Elizabeti. Nthawi imene Maria anapereka moni kwa Elizabeti, yemwe anali oyembekezera pa nthawiyo, mwana m’mimba mwake anadumpha ndi Chimwemwe. Elizabeti anali ndi kuthekera kodziwa chinthu chapadera chokhuza mwana yemwe Maria anali m’mimba mwake. Tikuyenera kudziwa

    izi zokhuza Elizabeti, iye anadziwa bwanji kuti Maria anali atayembekezera ambuye? Malemba amawonetsa kuti iye anali wodzadzidwa ndi mzimu wa mulungu. Izi zinapangisa kuti iye adzindikire bwino za mwana ameneyu. Chinthu chofunikira
    kudziwa ndi ichi, mulungu amachita zinthu zikuluzikulu myoyo yathu ngati ife timudalira iye ndi chikhulupiriro. Elizabeti anadalira mulungu moyo wake ndipo mulungu anamuzindikiritsa iye kuti Maria anali oyembekezera mpulumutsi wa anthu onse pa dziko. Maria yemwe anali ozichepesa pamaso pa mulungu anasankhidwa
    kubereka ambuye, zomwe ndi zinthu zopasa chidwi. Mulungu amagwiritsa ntchito anthu omwe ndi opanda kanthu kalikonse ku dziko kuti akwaniritse zolinga zake ndi kulemekeza zina lake. Mulungu amagwiritsa ntchito anthu omwe ndi opanda kanthu komanso ndi osaukitsitsa kuti achite zolinga zake ndi kulemekeza zina lake. Chimodzimodzi ife Akhristu lero, amene ndi osauka mu uzimu komanso opanda kanthu, mulungu angatigwiritse ntchito ngati timulora iye kuti atero. Choncho tiyeneni tizipereke kwa mulungu kwa tunthu kuti atigwiritse ntchito mu utumiki wake.   



    Luke 1:39-45 Mary visits Elizabeth. When Mary greets Elizabeth,

    who was pregnant at this time, the child in her womb made sudden movements showing happiness. Elizabeth is able to notice something special about the child Mary was carrying in her womb. There is something to be noted about Elizabeth, how was she able to know that Mary was carrying the lord in her womb? The scriptures show that she was filled with the holy spirit from God. This enabled her to know who this child was even before he was born. This makes Elizabeth’s child happy upon hearing the greeting from Mary. One thing important to take note of is that God can make great things in life happen to us but only if we
    believe in him and trusts him completely. Elizabeth trusted the lord and was given the privilege to know that Mary was carrying a child who literally would be the lord and savior of mankind. Mary from humble beginning was called by God to give birth to the lord, something which is remarkable. God uses those who are nothing in the eyes of the world to bring about his purposes and glorify his
    name. God uses people who are poor and lowly to accomplish his will and glorify his name. The same applies to us Christians who are lowly and poor in spirit, God can use us to accomplish his purposes and glorify his name. So we should be open and allow him to use us in his ministry.  

    36 min
  • Nkwabwino kukhala olimba muchikhulupiriro/It is good to remain firm in the Faith

    Luka 1:26-38 ikutibweretsera nkhani ya msungwana wosaziwa mwamuna otchedwa Maria ndipo amakhala mu zinda wa Nazareti ku Galileya. Msungwana ameneyu analibe kudziwika kulikonse, analibe chilichonse chopatsa chidwi komanso amakhala muzinda wosatchuka. Koma mulungu anali naye cholinga msungwanayu.

    Ngelo Gabrieli anabweretsa nkhani yabwino nati “uzakhala ndi pakati ndipo uzabereka mwana wamwamuna. Ndipo uzamutche Yesu.” Kubadwa kwa Yesu, kapena kunena kuti kubadwa kodzichepetsa kwa Yesu kunabwera kudzera mwa Maria. Koma mkati mwakukambirana ndi ngeloyo Maria anachita mantha. Izi zimachitika iye atalandira chitomero kuchokera kwa mwamuna otchedwa Yosefe wa fuko la Davide. Kukambirana kwawo kutatha Maria anamvetsetsa kuti ichi chinali chisankho cha mulungu ndipo iye sakanatha kutsutsa. Izi zinali motere chifukwa ankadziwa zina zokhuza mulungu. Zomwe ndizopatsa chidwi mukukambirana kwawo ndi momwe Maria anamuyankhira ngeloyo. Iye anati “zichitike monga momwe mwanenera. Popeza ine ndi mtumiki wa ambuye.” M’mawu ake, iye akuwonetsa kukula kwa chikhulupiriro chake pa mulungu. Iye akutiphunzitsa kulemekeza zisankho zomwe mulungu amatipangira ife ngati ana ake komanso osankhidwa ake. Monga ana a mulungu, ngakhale tikumane ndi mavuto oopsa, titsatire chitsanzo chabwino cha chikhulupriro cha Maria. Tikhale ndi mtima okwanitsa kunena kuti ‘zikhale monga momwe ambuye mufunira.’


     

    Luke 1:26-38 brings us a story of a young virgin named Mary who lived in a small town of Nazareth in Galilee. This young woman had no publicity, had nothing interesting and was living in a place not famous. But God had a plan for her. Angel Gabriel brought her news saying “you will be pregnant and give birth to a son. And you will name him Jesus.” The birth of Jesus, also known as a humble birth of Jesus came about through this young woman called Mary. In the midst of all this, Mary was terrified and was afraid. At this point already, she had received a marriage proposal from a man called Joseph of the clan of David. After conversing with angel Gabriel, Mary finally understood and agreed to it, for this was God’s choosing and she had no objection. This was so, because she understood things concerning God. What’s interesting is how she responded to the angel. She said to the angel ‘let it be as you have said, for I am the servant of the lord.’ In her words, she expressed a tremendous amount of faith in God. She teaches us how to value the choices that our creator makes for us as his chosen ones and his children. As the children of God, in every circumstance that we face whether good or bad in his ministry, we should imitate Mary’s faith. We should learn to say that ‘let it be as the lord has purposed it.’

    53 min
  • khalani anthu okonda chilungamo/Be a people that love justice

    Mateyu 5:21-26 ikupitiriza kuyankhula zokhuza chilungamo. Ndipo chilungamo chimene mulungu akufuna, sichakunja ayi koma chankati mwa munthu. Yesu akuyankhula kunena kuti ‘ngati chilungamo chanu sichiposa cha afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, simuzalowa mu ufumu wakumwamba.’ Mu zoyankhula zina,Yesu akuyamba mayankhulidwe ake kunena kuti “munamva kunanenedwa kuti.” Kuchoka pamenepo iye akuyankhula ndi kuwaonetsa anthu zokhuza chilamulo cha Mose. Komanso akuwawonesera momwe angatsatirire chilamulo chimenechi. Kenako akubwerera ku nthawi yatsopano kuti afotokoze momwe amayenerera kumvetsetsera chilamulo chimenechi. Kodi ndi zofunika bwanji kuti iye akambe zimenezi? Yesu watiwuza kale kuti sanabwere kuzathetsa chilamulo ndi aneneri koma kuzakwaniritsa. Yesu akutiwuza kunena kuti chilungamo chanthu chisangokhala cha kunja kokha koma chizichokera mkati mwathu. Potengera ndi zomwe chilamulo chimafuna kuti tizichita,

    ndi Yesu yekha amene anakwaniritsa kukhala moyo omvera chilamulo chimene mwangwiro. N’chifukwa chake akutiwuza momwe tingatsitirire chilamulo chifukwa iye ndiye amene akudziwa bwino lomwe. Yesu akutipempha kuti tikhale anthu
    okonda chilungamo. Ndipo chilungamo chathu chiwale ngati muni kuti onse omwe awona kuwalako alemekeze atate athu akumwamba. Chilungamo chathu chisakhale chakunja kokha kuti ena atitamandire ife.

     

     

    Matthew 5:21-26 continues to talk about justice. And the type of justice that God wants, is not the outward justice but the inward justice. Jesus makes a statement about this saying that ‘if your righteousness does not surpass that of the Pharisees and the teachers of the law, you will by no means enter the kingdom of the heavens.’ Now, in his statements, Jesus begins most the sentences with the word “you heard that it was said.” And from there, he goes back to the old testament and show people what the law of Moses is about and also show them how they should live by it. And then he goes back to present time and show the people how they should understand the law of Moses. How important is it that he explains the law? Earlier, Jesus has already told us that he didn’t come to abolish the law and the prophets but he came to fulfil it. So, Jesus shows us that justice shouldn’t be a thing of outside but should involve inside life. And looking at what the law requires us to do, the only one who can follow the law perfectly is Jesus. Jesus in his entire life lived in obedience to the law. And that is why he tells us how to follow the law because he knows how. Jesus invites us to exercise true righteousness. Let it shine like light before men, and those who see it will glorify our heavenly father. Our righteousness shouldn’t be a thing of outside appearance in order to be praised by others.

    50 min
  • Yesu aphunzitsa ndi ulamulilo/Jesus teaches with authority

    Mateyu 7:24-29 Yesu akuyamba vesi 24, kunena kuti ‘yense omva mawu anga.’ Izi ndizofunika kuzisunga, chifukwa zithandizira ife kumvetsa bwino chifukwa chimene anthu omvera ulaliki wake ananena kuti amayankhula ngati yemwe anali ndi ulamuliro. Osati ngati aphunzitsi amalamuliro. Anthu ambiri analondola Yesu. Ndipo iye anakwera paphiri nayamba kuphunzitsa ophunzira ake. Mu mavesi a 24-29, yesu akuyankhula za munthu wanzeru ndi opusa. Awafotokoza motere; munthu wanzeru ndi amene amamva mawu ake ndi kuwachita. Kenako akulumikizisa ndi munthu yemwe akumanga nyumba yake pa tanthwe. Mvula inabwera koma nyumba sinagwe chifukwa inamangidwa polimba. Njira iyi ndi yomwenso Akhristu akuyenera kugwiritsa ntchito kumanga chikhristu chawo. Akhristu akuyenera kumanga pa tanthwe limene ndi Yesu Khristu. Ndipo iye akulonjeza kuti ndi maziko omwe sadzagwetsedwa konse. Ndipo pamapeto iye akumaliza ndi munthu opusa. Munthu opusa akumanga nyumba yake pa mchenga. Mvula inabwera ndipo nyumbayi inagwa. Zitsanzo zonsezi zimamveka bwino kunena kuti, wanzeru ndi munthu amene amamva mawu a Yesu ndi kuwachita ndipo munthu uyu ndi odala, Mateyu 5. Izi ndi zosiyana ndi munthu yemwe amamva mawu a Yesu ndipo samawachita. Zimangowonetsa kuti munthuyu sanamve konse mawu a Yesu. Ndiponso munthuyu sanali Khristu kumayambiriro komwe. Ndipo izi zimamupanga iye kukhala munthu opusa. Mayankhulidwe oterewa ndi omwe angayankhulidwe ndi yemwe ali ndi ulamuliro. Ndi chifukwa anthu anati, akuyankhula ngati munthu yemwe ali ndi ulamuliro osati ngati aphunzitsi amalamulo.

     

    Mathew 7:24-29 Jesus begins verse 24, saying ‘whoever hears my word.’ Now, we have to take note of this because that will help us to understand why the crowd listening to him concluded saying that ‘he spoke as someone with authority. Not like the teachers of the law.’ A huge crowd followed Jesus. And Jesus gets on a mountain and sits down and opened his mouth to teach his disciples. In verses 24-29, Jesus talks about someone who is wise and someone who is foolish. He describes them this way; a wise person is the one who hears his word and does it. And from there he links it with someone who builds a house on a rock. Jesus said that, the rains came, the wind blew and the flood water lashed against this house but it was founded firm and it remained. And this applies to how true Christians are to build their houses

    which is their Christianity. Christians are to build on the true foundation which is Jesus Christ. And Jesus assures his people that no matter what problem they may face, they never will be destroyed for they are founded on the true foundation which is Jesus. And finally, Jesus concludes talking about a foolish person. Now, this person is foolish because he builds his house on sand and the rains come and lashes against this house and it is destroyed. Now all these two examples are understood clearly this way; Jesus talks about his word, the one who hears his word and does it is blessed, Matthew 5. in simple terms, this person hears and does it and is a happy person. This is unlike with someone who hears and does not do Jesus word. In simple terms, it just shows that this person never heard the word of Jesus. And never was a Christian to begin with, this makes that person a fool. It is only someone with authority who can speak like that, thus why the people concluded that he spoke like someone with authority not like the teachers of the law.

    39 min
  • Mzimu woyera anatsekulira njira anthu amitundu kuti akhulupirire uthenga wabwino/The holy spirit opened the door for gentiles to believe the Gospel

    Mateyu 5:17-20 Yesu akwera pa Phiri ndipo akhala pansi ndikuyamba kuphunzitsa ophunzira ake ngati Mose watsopano ndi opereka lamulo watsopano. Funso nali, funso limene limazunguza anthu ambiri; kodi ndi ubale wanji omwe ulipo pakati pa lamulo la Khristu ndi la muchipangano chakale? Pofuna kuyankha funso limeneli, chiyambi cha vesi ya 17 ya chaputachi imapereka yankho lomveka bwino. Yesu anti “musaganize kuti ndinabwera kuzathetsa chilamulo ndi aneneri. Sindinabwere kuzathetsa koma kudzakwaniritsa.” Tsopano, chaputa cha 1, 2, 3, 4 cha Mateyu muli zolemba zomwe zimasonyeza kukwaniritsidwa kwa kubwera kwa Mesiya. Mwa chitsanzo, mwana Yesu anatengeredwa ku Igupto pofuna kukwaniritsa zomwe zinalembedwa zonena kuti ‘ndinamuitana mwana wanga kuchoka ku Igupto.’ Izi zikuonetsa kuti Yesu sanabwere kuzathetsa chilamulo ndi aneneri koma kuzakwaniritsa zonse zomwe zinalembedwera iye, zokhuza iye. Koma, kodi chilamulo, aneneri ndi zolembalemba zinangoperekedwa kwa Ayuda popanda chifukwa? Kapena inangokhala njira yonena kuti iwo azizitukumulira? Ayi! Chilamulo komanso aneneri zinaperekedwa kwa iwo ngati njira yowakonzekeretsa za kubwera kwa Mesiya. Ndiye, tinene kuti chilamulo ndi aneneri zikuphunzitsa ife kuti tizinyoza ena omwe samatsatira kadyedwe ka Ayuda? Kapena chifukwa samapembeza tsiku lofanana ndi lomwe inu mumapembezera? Kapena chifukwa samasunga sabata momwe inu mumachitira? Yesu akutitsimikizira kuti anabwera kuzapulumutsa Ayuda ndi Amitundu. Izi zikuoneka bwanji? Mzimu woyera amatsekulira njira amitundu kuti amve ndi kukhulupirira uthenga wabwino wa Yesu Khristu ndikulandira chipulumutso.


     

    Matthew 5:17-20 Jesus gets on a mountain and sits down to teach his disciples as the new Moses and the new law giver. Now the question that has many people wonder so much is; what is the relationship of the law of Christ to the law of the old testament? To answer that question, the beginning of verse 17 of this chapter clears our minds with what Jesus himself said. Jesus said “don’t think that I came to abolish the law or the prophets. I did not come to abolish but to fulfill.” Now, chapters 1, 2, 3, 4 of Matthew records all the accounts that took place in fulfilment of the coming of Messiah. For example, baby Jesus was taken to Egypt to fulfill what was written saying that ‘I called my son out of Egypt.’ This shows us that Jesus indeed came to fulfill what was written about him and for him and not to abolish the law and the prophets. But, was the law, the prophets and the writings given to the Jews for no good reason at all? Or was it just for them to brag that they had the law and the prophets? No! the law and the prophets were given them as a way of preparing them for the coming of messiah. So, does the law and the prophets teach us to view others lesser because they’re unable to follow the diet of the Jews? Or because they do not worship on a certain day like you do? Or that they do not keep the Sabbath according to your point of view? Jesus tells us clear that he came to save all, whether Jew or Gentile. Where do we see this? The holy spirit opens the door for Gentiles to hear and believe the Gospel of Jesus Christ and receive salvation.  

    50 min
  • Kumwalira kwa Sara/The death of Sarah

    Genesis 23:1-20 ikukamba za nkhani yokhuza imfa ya Sara mkazi wake wa Abrahamu. Chaputachi chikuwonetsera momwe Sara anali ofunikira komanso kunali koyenera bwanji kulemba za imfa yake mu bukhu lopatulika. Tikayang’ana m’machaputa ambuyo pamene Abrahamu amayitanidwa ndi mulungu, tipeza kuti anachoka kwawo pamodzi ndi Sara komanso Loti. Tinaonanso momwe moyo wa Loti ndi banja lake unathera. Koma kudzanja linali, posatengera mavuto omwe Abrahamu amakomana nawo sanali yekha. Nthawi zonse iye amakhala ndi mkazi wake Sara. Sara anali ndi chikhulupiriro ndipo anawelengera malonjezo omwe mulungu anapanga. Ndipo kumapeto a moyo wake anawona limodzi mwa malonjezo a mulungu akukwaniritsidwa. Sara anabereka mwana ali ndi zaka makumi asanu ndi anayi. Iye analandira lonjezoli pamodzi ndi Abrahamu. Ndi kudzera mwa iye mbewu ya mzimayi inayamba kuzafikira pamene Yesu Khristu anabadwa. Iye ndi chitsanzo chabwino kwa azimayi omwe ndi Akhristu ndipo ali m’mabanja masiku ano. Sara anakhalabe ndi Abrahamu nthawi zonse za moyo wake, iye anatsatira Abrahamu ngakhale sankadziwa komwe amapita ndipo anakhala mumatenti nthawi yambiri ya moyo wake ndipo sanadandaule kanthu konse. Izi zikuyenera kulimbikitsa azimayi omwe amuna awo ndi otumikira ndi kulalika uthenga wa Ambuye Yesu. Thandizani

    amuna anu momwe anachitira Sara ngakhale mutakhala kuti simukuona tsogolo lililonse, athandizenibe chifukwa izi zimakondweretsa Ambuye wanu wamkulu Yesu Khristu.


     

    Genesis 23:1-20 tells us a story of the death of Sarah the wife of Abraham. This chapter also shows us how and why Sarah was important and it was worthy to record her death in the bible. If we go back to when Abraham was called, we would find out that he went out of his land accompanied by his wife and Lot his nephew. We saw how it ended for Lot and his family. But on the other hand, despite all the hardships Abraham faced, he was not alone. He was always with his wife Sarah. Sarah was firm in the faith and counted on the promises God made. And at the end of her life she witnessed one of the promises made by God being fulfilled. She gave birth to a son at the age of 90 after many years of no children. After God promised her a child, she lived to see that along side her husband. And it was finally witnessed by both of them and through her the seed of a woman was made manifest down to the birth of Jesus Christ. This plays out a good example to Christian women in todays time. Sarah stayed with her husband throughout all that God commanded them to do. She went out of her home with him without knowing where they were going. She stayed in tents many days of her life yet she worried not of prestige. This should encourage Christian women whose husbands go out to minister to others and preach the gospel. Support your husband just like Sarah did even when you see no hope, keep on supporting your husbands for this is pleasing to the lord.


    35 min
  • Akhristu ndi mchere wa dziko lapansi/Christians are salt of the world

    Mateyu 5:13-16 ikutionetsa kuti makhalidwe ankhristu mu dziko lapansi alingati mchere wa dziko lapansi. Makhalidwe a akhristu, momwe amayankhulira ena komanso momwe achitira ndi ena

    zilingati kuwala komwe kuwunikira dziko lapansi. Mu chaputa 5, tikupeza zinthu ziwiri zomwe ndi zofunika pa moyo wa anthu pa dziko lapansi. Izi ndi monga mchere komanso kuwunika. Tikhoza kukhala opanda suga koma ndikuphika phala kuthira mchere anthu ndi kudya phala opanda chodandaula chilichonse. Munthu
    uthakukhala opanda mafuta ophikira kapena tomato koma ndi kuwilitsa nsomba ndi kuthira mchere anthu ndi kudya opanda vuto lilonse. Zitsanzo izi zikuonetsera momwe mchere uli ofunikira. Momwenso kuwunika, kuwunika ndi kofuna pa moyo wa
    munthu. N’chifukwa palibe amayatsa nyali ndi kuyivindikira ndi mbiya koma amayisiya poti iwalile aliyense pamalopo. Anthu amafuna kuwunika nthawi zonse chifukwa anthu amadana ndi mdima. Ndi malingaliro amene, Yesu akulangiza ophunzira ake kuti nawonso akhale ofuna kuwonetsa makhalidwe abwino omwe
    watchula kale monga kuleza mtima, kukonda mtendere ndi zina zambiri. Muvesi ya 16, Yesu akumaliza ndi kunena kuti “momwenso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwinondi kulemekeza atate anu akumwamba.” Pamene mukonda ena posatengera mkwiyo wawo painu, pamene mukonda ena pamene adana nanu, anthu azaona ndipo azalemekeza atate anu akumwamba.



    Matthew 5:13-16 is showing us that the way Christians conduct themselves in the world is like salt of the world. The attributes of Christians, how they speak with others should be like the light shining forth in the world. In this chapter we are finding out two

    things that are very essential to humans and they cannot live without them. These things are salt and light. We can be without sugar and yet cook porridge and only add salt and have people eat. You have no cooking oil and tomatoes but still boil fish and only add salt to it and have people eat. These examples demonstrate how important salt is to the survival of human beings. Same applies to light, humans cannot live without light. This is why no one lights a lump in a house and covers it with a basket but instead puts it where it shines on all those in the house. Humans always want to be where there is light, we dislike darkness very much. With that in mind, Jesus is telling us that it should be the same with the followers of Jesus Christ. The followers of Jesus Christ should show all the attributes Jesus has already spoken about in the verses before these verses. Attributes like humbleness, peacemakers and many others. Now Jesus tells us why it should be like that at the end of verse sixteen. He
    says “let your light shine before others, so that they may see your good works and give glory to your father in heaven.” Yes, when people see you loving others despite their hating you, when they see you loving peace despite others criticizing you, they know and see the love for God that is within you. And will glorify your heavenly father.

    54 min
  • Moyo wa Chikhulupiriro wa Abrahamu/a life of Faith of Abraham

    Genesis 22:1-2 ikuyamba ndi yesero. Yesero lomwe ndi lovuta kukwaniritsidwa. Mu vesi yachiwiri ya chaputa chimechi, mulungu akuonetsera momwe kunali kovuta kukwaniritsa yeseroli. Zaka zambiri zadutsa, mulungu wachita zomwe analonjeza kuti achitira Abrahamu. Mulungu wapereka mwana kwa Abrahamu ndi Sara ndipo amutcha Isaki. Mu chaputa 22 cha bukuli tikuona mulungu akumuuza Abrahamu kuti apereke nsembe mwana wake Isaki. Izi zinali zovuta kuchita osati chifukwa Abrahamu anali ndi Isaki yekha (analinso ndi Ishumaeli) koma ndi kudzera mwa Isaki m’mene mulungu adzakwaniritsa ntchito yake ya chipulumutso. Komanso Abrahamu amamukonda Isaki. Abrahamu wavomera kuchita chifuniro cha mulungu. M’malingaliro mwa Abrahamu munali buku la Ahebri lomwe limakamba za chiwukitso. Izi zinapereka mphamvu kwa Abrahamu. Pa ulendo wawo kupita kopereka nsembe Isaki anafunsa bambo ake funso lachodziwadziwa ndipo yankho la funsoli likuonetsera chinthu chofunika chokhuza mulungu. Abrahamu anati “mulungu akapereka.” Pamene Abrahamu amafuna kupha Isaki kuti ampereke nsembe mulungu anamulesa. Ndipo mulungu anapereka mwana wa nkhosa kuti aperekedwe nsembe. Kodi izi zikukamba zotani zokhuza mulungu? Tonse ndi anthu ochimwa amene tikuyenera imfa. Koma mulungu anapereka nsembe osati ya nyama koma ya mwana wake yemwe kuti aphedwe m’malo mwathu. Ngati zotsatira mulungu akupereka chipulumutso kwa anthu ake kudzera mwa mwana wake Yesu Khristu. Kodi inu mukudalira mulungu kapena mumamukaikira? Tiyeni tikhale moyo wa chikhulupiriro momwe anachitira Abrahamu.



    Genesis 22:1-2 begins with a test. A test that is too hard to carry out. God in verse two of this chapter makes it clear that all should understand how difficult it is to do what God was asking here. Many years have passed, God has carried out what he had promised. God has given Abraham and Sarah a child and they have named him Isaac. In chapter 22 of this book we see God asking Abraham to do something difficult. He tells him to sacrifice his son Isaac. Now this was difficult for him to do not because Isaac was his only son (he had Ishmael) but was the one through which God would accomplish his plans of salvation. And Abraham loved Isaac very much. Abraham agrees to this and is ready to sacrifice his beloved son. Abraham was strengthened thinking about what is written in the book of Hebrews which says

    that God has the power to bring someone dead back to life. But something unique happened on his way to sacrifice Isaac. Isaac asks his father an obvious question and the answer to that reveals something important about God. Abraham responds to his son saying “God will provide.” This was not a lie but in fact the truth. When he was about to kill his son Isaac and sacrifice him God stopped him. And he provided a ram for the sacrifice. Abraham had passed the test. What does this say about God? We all are sinners and deserves to die. But God provided a sacrifice of his own son to die in our place and give us his life. As a result, God is giving salvation to his people through Jesus Christ. Do you trust God or are you still doubting him? Let us live a life of faith like Abraham did.

    29 min
  • Chinthu chabwino chochokera kuchoyipa/A good thing that comes from a bad thing

    Mateyu 5:11-12 Yesu wasintha chidwi chake tsopano. Iye akuuza ophunzira ake kuti ndinu odala pamene anthu akunyozani kapena kukuzunzani. mu mavesi omwe abwera mosogozana ndi awiriwa, Yesu wakhala akugwiritsa ntchito mayankhulidwe akuti ‘odala ndi amene’ koma tsopano mumavesi awa iye wayamba ndi mawu akuti ‘odala ndi inu.’ M’mayankhulidwe otere, Yesu akuyankhura ndi ophunzira ake kuphatikizira iye mwini. Iye akuwatsimikizira kuti monga iwo ndi ophunzira ake, azazunzidwa, anthu azalimbana nawo ndipo ena mwa iwo azaphedwa chifukwa cha Yesu Khristu. Koma kodi akuyenera kudandaula ndi zimenezi? Ayi! M’malomwake Yesu akuwawuza kuti amakhala osangalala pamene izi ziwachitikira. Yesu akumaliza m’mavesi awiriwa motere “sangalalani ndipo kondwerani, popeza mphoto yanu ndi yayikulu kumwamba. Chifukwa momwenso ndi momwe anazunzira aneneri inu musanabwere.” Okhulupirira weniweni chidwi chake chimakhala pa mphoto imene Yesu akuyankhula mumavesi awa. Ndipo imayenera kumupanga kukhala osangalala. Izi zimaperekanso mphamvu kwa onse omwe akuchitira umboni wa Yesu kumaiko omwe amalesa kutero. Izi zimawapangitsa kularikira molimba mtima.


     

    Matthew 5:11-12 Jesus has now shifted his focus. He now tells his disciples that happy are you when people say bad things about you or persecute you. In verses preceding these two verses, Jesus has only used this language ‘happy are those’ but now for a change he says ‘happy are you’ referring to his disciples even including himself. In simple terms, Jesus assures his disciples and even his followers that they will be persecuted and people will go against them and even kill them because of Jesus Christ. But should they despair because of this? No! Instead Jesus tells them that they are happy when that happens to them. Jesus concludes these two verses by saying that “be glad and rejoice, because your reward is great in heaven. For that is how they persecuted the prophets who were before you.” One who is a true believer focuses much on the prize that Jesus speaks of in the Bible and that is what should make him/her happy. This is also a way of drawing strength, especially to those who are in countries which opposes the witnessing of the suffering of Jesus Christ. This should make them bold in preaching the gospel in such countries.

    39 min

About Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

From the publisher's feed

Sermons and teaching in Chichewa and English

More shows like Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Gospel Life | Malawi, Missions, and More by Josh Hutchens & Isaac Dzimbiri | Gospel Life

Gospel Life | Malawi, Missions, and More

12 Listeners