Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Download on the App Store

Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine episodes

  • Abrahamu kapolo wodzipereka/Abraham a devoted servant

    Genesis 21:22-33 padutsa kanthawi tsopano, Abrahamu wapita

    ndikukhala ndi a filisti. Ndipo kumeneko anakumana ndi Abimeleki. Abrahamu adamuuza Sara kuti azinena bodza kuti anali mlongo wake wa Abrahamu. Izi zinatheka, komabe mulungu anawululira Abimeleki bodza lomwe anawuzidwa chifukwa anali atatenga Sara kukhala mkazi wake. Mulungu sanakondwere ndipo anapangitsa azimayi onse akufilisti kukhala osabereka. Kenaka mulungu mwini analowererapo ndipo anawonesera vuto kwa Abimeleki. Abimeleki anapita ndikukakambirana ndi Abrahamu ndipo iye anapemphera kenako themberero linachotsedwa. Zotsatira zake Abimeleki anachita pangano ndi Abrahamu ndipo zinayenda bwino. Pangano litachidwa ndi anthu awiriwa ku Berisheba, Abrahamu anadzala mtengo komweko. Abrahamu anapembeza ambuye pansi pa mtengo. Abrahamu akuwonesera munthu yemwe ndi wodzipereka kwatunthu kwa mulungu. Tikumuona akudzala mtengo, ndipo pansi pa mtengo iye akupembeza ambuye. Nthawi zonse iye amakonda kupemphera. Iye ndi chitsanzo chabwino. Timadziwa kuti tazunguliridwa ndi mphamvu za kumidima zomwe sitingamenyane nazo ndi thupi
    ndi magazi athu. Mulungu yekha ndi amene angamenyane nazo. Ndipo ife tiyenera kukhala okonda kupemphera nthawi zonse.

     

    Genesis 21:22-33 it has been a while now, Abraham has gone

    and live with the Philistines. And there he met with Abimelech. Now Abraham had told Sarah his wife to lie saying that they were brother and sister. It worked out, but later God reveals to Abimelech the lie that Abraham had told him for Abimelech had taken Sarah as his wife. God was unhappy and he caused the women of the city to become barren. Then God intervened and revealed the problem to Abimelech and afterward Abraham prayed to God and the curse was lifted. As a result of this Abimelech enters a covenant with Abraham and it worked out beautifully. Now, after the promise was made between the two at Beersheba, Abraham planted a tree there. Abraham worshiped the lord there. Abraham is demonstrating the life of someone who is highly devoted to God. We see him planting a tree, and there he
    worships the lord. He stays prayed up all the time. This is a good example. We know today that we are surrounded by powerful forces we cannot fight with flesh and blood, and the only one who can fight them is God himself. So, the best thing we can do is to pray constantly.  

    41 min
  • Odala ndi amene azunzika chifukwa cha Chilunngamo/Happy are those who suffer because of Righteousness

    Mateyu 5:10 ikutiwuza ife kuti madzi osefukira akubwera kutsogolo kwathu. Yesu akutichenjeza za madzi osefukirawa. Ndipo akutiwuza kuti palibe yemwe angakwanitse kuthawa madzi osefukirawa. Njira yokha imene munthu ungathawire madzi osefukirawa ndi pamene uli ndi madziko angwiro. Madziko amenewa amatsindika ngati tili okondwa tsopano chifukwa cha zomwe zizachitikira ife kutsogolo. Izi ndi zimene zikulumikiza mathero a chiphunzitso cha paphiri ndi chiyambi cha chiphunzitso cha paphiri. Anthu amene ndi odala tsopano, amene amadziwa Chimwemwe chenicheni ndi anthu amene ali ndi chiyembekezo chopirira madzi osefukira omwe akubwera kutsogolo. Madzi osefukira omwe ndi nkwiyo wa mulungu ukamatsulidwa, ndani angayimirire pamaso pake? Zomwe ndi zoona kutsogolo zimatsimikizira Chimwemwe chathu lero. Zotsatira zake tinganene kuti Chimwemwe chenicheni ndi pamene ukhala otsatira wa Yesu Khristu. Munthu wake ndi amene amamva mawu a Yesu ndi kuwachita.    

     

     

    Matthew 5:10 is telling us of a flood that is coming ahead of us. Jesus warns us of this storm. And he tells us that it’s coming for us and nobody can escape it. The only way to escape it is to endure the storm. How? By having a strong foundation. This foundation can determine whether we be happy now regarding what will happen to us in the future. And this is the connection between the end of the sermon on the mountain and the beginning of the sermon on the mountain. The people who are blessed now, people who know true happiness now are the people who have the hope of enduring the storm that is coming. When the flood of the judgement of God is unleashed, who will remain standing? What is true in the future is what should determine our happiness today. Therefore, we can say that true happiness is to be a disciple of Jesus Christ. It truly means to be someone who hears the word of Jesus and take your life and align it with Jesus’ word.

    45 min
  • Osankhidwa ndi mulungu ndi okanidwa ndi mulungu/The chosen ones of God and those rejected by God.

    Genesis 21:8-13 ikufotokozera zinthu ziwiri zofunika kwambiri, zinthu zimene zikuchitika pa dziko lapansi, m’mabanja ingakhale mu mpingo. Tikuwona nkhondo imene ikuchitika pakati pa osankhidwa a mulungu ndi onse omwe ndi okanidwa ndi mulungu. Koma kuti timvetse bwino izi, chaputara 3 cha bukuli chikutipatsa kumvetsetsa kwakulu. Mulungu akuuza njoka ija kuti “ndizayika

    chidani pakati pako ndi mzimayi, pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Iye azaphwanya mutu wako ndipo iwe uzaluma chitendeni chake.” Izi zikuoneka pamene Adamu ndi Hava abereka ana awiri amene anali Kaini ndi Abere. Ana awiri awa anapereka
    nsembe kwa mulungu ndipo mulungu anavomera nsembe ya Abele ndikukana nsembe ya Kaini. Mulungu akusankha Abele ndikukana Kaini. Ndipo mapeto ake Kaini anapha m’bale
    wake. Izi zikupitirirabe kufikira nthawi ya Isaki. Ana a Ishumaeli akukula ndikumalimbana ndi ana a Isaki. Izi ndi zofunika kumvetetsa bwino chifukwa; izi zikukwaniritsa lonjezo limene mulungu anapanga mu chaputa 3:15 cha bukuli. Mu buku lopatulika muli malonjezo ambiri amene akukwaniritsidwa munthawi yathu ino. Izi ziyenera kutipatsa chilimbikitso ndi kukhala opilira mu chikhulupiriro chathu mwa Yesu Khristu.


    Genesis 21:8-13 introduces us to two things that are much greater, things that are still happening throughout the entire world, in families and even in the churches. We see war between two kinds of people, those who are chosen by God and those who are rejected by God. But for us to understand this war better, chapter 3 of this book gives us a much wider understanding of this problem. God tells the serpent that “I will put hostility between you and the woman, between your offspring and her offspring. He will strike your head, and you will strike his heel.” This is evident when two brothers are born to Adam and Eve, Cain and Abel. These two offered up sacrifice to God and God accepted Abel’s sacrifice but rejected Cain’s. Thus, choosing Abel and rejecting Cain. Later Cain kills his brother. This happens throughout until the birth of Isaac. Later we see the descendants of Ishmael fighting against the descendants of Isaac. Now this is important to note of because; it is the fulfilment of the prophecy in Genesis 3:15. The bible contains many prophecies that are seeing fulfilment today and this should give us courage and remain bold in professing our faith in Christ.

    44 min
  • Ambuye achitira Sara zomwe adalonjeza/The lord did for Sarah what he had promised

    Genesis 21:1-7, zaka 25 zadutsa kuchokera pamene mulungu anapanga malonjezo ake kwa Abrahamu komanso Sara kuti azawapatsa mwana. Abrahamu wakwanitsa zaka 100 ndipo Sara wakwanitsa zaka 91. Kuthekera kosonyeza kuti awiriwa angakhale ndi mwana sikumasonyeza. Sara wadutsa zaka zoberekera mwana. Koma funso nkumati, kodi chilipo chomwe chingamukanike mulungu? Tikudziwa kuti mulungu amasunga mawu ake komanso amakwanilitsa malonjezo ake munthawi

    yoyikika, ukulu wa mulungu ndi kukhulupirika kwake sikuwona malire. Koma kudzera mu moyo wonse wa Abrahamu tawona kuti kusamvera mulungu kumabweletsa mavuto. Koma kodi izi zingaletse kukwanilitsidwa kwa malonjezo a mulungu? Ayi. Chifukwa ninji? Mulungu ali ndi kuthekera kosintha mavuto kukhala Chimwemwe. Sara anadikira kwa nthawi yayitali komanso analandira chitonzo chokhala munthu osabereka. Koma
    tikuona mulungu akukwanilitsa malonjezano ake ndipo Sara akubereka mwana. Nthawi ingatalike bwanji kapena ingafupike mulungu amakwanilitsa malonjezano ake.

     

     

    Genesis 21:1-7, 25 years have passed since God made his promise to Abraham and Sarah to give them a child. Abraham has turned 100 years and Sarah has turned 91 years old. We can just imagine the impossibility of these too having a baby per God’s promises. Sarah has passed the age of child bearing. But the question is, can there be anything too extraordinary to God? We know that God keeps his word and fulfils his promises at the pointed time, God’s sovereignty and faithfulness see no boundary. But through out the

    life of Abraham we learn some valuable lessons like our disobedience to God brings us sorrows. But can that stop God’s promises from being fulfilled? The answer is no. Why? Because God has the ability to turn calamities into happiness. Sarah waited for so long and she suffered as well the taunts of being barren. But
    we see God finally fulfilling his promise and Sarah nurses a baby. It does not matter how far or how long, come what may God still fulfills his promises.

    33 min
  • Tchimo silisintha kukhala choonadi/ A lie cannot change to be the truth

    Genesis 20:1-18 mukumvetsetsa kophweka, mu ndime ya malemba iyi ikutithandiza kumvetsa kuti palibe choona chilichonse chimabwera kuchokera ku bodza lonenedwa ndi Khrisitu. Palibe chomwe chingabise machimo pamaso pa ambuye machimo akachitidwa. Mu ndime ya malemba iyi ikutionetsera

    kuti tchimo silingasinthidwe kukhala chinthu chabwino. Tikuona Abrahamu akunena bodza kawiri konse kuyambira pomwe anayitanidwa ndi mulungu. Koma kodi izi zikumupangitsa kukhala olondola? Bodza lakuti Sara anali mlongo wake linalibe
    chophimba chilichonse pamaso pa mulungu ngakhale linapulumutsa Abrahamu kwa kanthawi kochepa chabe. Koma mulungu akutionetsera kuti Abrahamu analakwitsa ponena bodza. Mulungu akumuonesera mfumu Abimelech bodza lomwe Abrahamu wanena. Izi zikusonyeza kuti mulungu sanagwirizane nazo zomwe iye anachita ponena bodza. Nthawi zambiri Akhrisitu amayesera kunena zomwe amatchula kuti ndi bodza
    loyera pofuna kuzipulumutsa kuzoopsa. Koma mulungu akutionesera apa kuti kulibeko bodza loyera. Tingoyenera kumudalira ndi kukhulupirira iye nthawi
    zonse. Ndipo pamene tipepesa, tisangonena pamwamba chabe. Mulungu amadziwa zonse zomwe tachita komanso tachita chifukwa chiyani. Tingoyenera kudzindikira tchimo lomwe tachita ndi kulapa kuchokera pansi pa mtima.



    Genesis 20:1-18 in simple terms, this chapter helps us

    to understand that there is no truthfulness in any white lie that can be told. All sins are inexcusable before the lord. In this chapter we come to realization that no sin that can be told can be justified to be right. We see Abraham telling the same lie twice now since his calling. But does this make him right? The lie that Sarah was his sister was without excuse though it seemed to have given Abraham a temporary safety. But God shows us here that it
    was never apart of his plan for Abraham to tell a lie. God comes and reveals the lie to king Abimelech showing us that he is against the lie Abraham had told. They’re times that Christians try to tell what they call a white lie in order to save themselves from danger. But God here tells us that there is no such thing as a white lie. All we need to do is to trust him always. And when we make a mistake, it isn’t right just to give a surface apology to God like
    others do. He knows what we have done and how we did it, and he expect us to know our mistake and confess to him and then we apologize.  

    42 min
  • Ana a mulungu amabweretsa mtendere/Children of God brings peace

    Mateyu 5:9 tikupeza phunziro lofunika mu ndime imeneyi. Ndime ya malemba yosatizana ndi iyi ikukamba za kuyera mtima. Kodi ndi ndani yemwe ali oyera mtima? Munthu yemwe samazifunira ulemelero iye mwini, munthu yemwe samapembeza mafano ndipo amadana ndi tchimo momwe atate ake akumwambwa amadanilana ndi tchimo. Yemwe achita zimenezi amakhala osangalala, chifukwa? Otero azamuona mulungu. Maganizo omwewo akutithandiza kumvetsa bwino za mfundo yobweletsa

    mtendere. Ana a mulungu amabweletsa mtendere. Tikuyenera kudziwa kuti kutengera mu chikhalidwe cha munthu, palibe yemwe angabweletse mtendere payekha. Munthu amangokhumbira chisokonezo ndi kukhala chopunthwitsa ena. Koma mulungu ndi yekhayo amene angabweletse mtendere. Ndipo yemwe ali mwa mulungu, ndi yemwe angabweletse mtendere chifukwa mulungu akuonesera mtendere wake mwa munthu ameneyo.   


    Matthew 5:9 we find a very valuable lesson in this passage. The preceding verse, verse 8 talks about being pure in heart. Now, who are those pure in heart? Those who don’t desire to bring honor to themselves, they don’t do idol worship and they hate sin just as their heavenly father hate sin. These are called happy because they are pure in heart and what will happen to them? They will see of God. Now with that in mind, verse 9 speaks about

    children who bring peace and these are children of God. But we need to understand that according to our human nature, we cannot bring peace. We love to bring chaos and be a stumbling block to others. It is only God who brings peace. And obviously speaking, if you are in God then we can rightly say you have the possibility to bring peace. As a result, through you God brings about peace.

    44 min
  • Moyo olekana ndi mulungu ndi mavuto okhaokha/Life apart from God equals suffering

    Genesis 19:30-38 ikumaliza ndi mathero a Sodom ndi Gomora. Bukhu lopatulika molungama limanena za mbiri ya anthu (kuphatikizirapo zoofoka zawo ndi momwe zimawonjezera ku mavuto awo). Mu ndime yamalembayi, tikupezamo phunziro lofunika kwambiri; moyo olekana ndi mulungu ndi mavuto

    okhaokha. Anthu okhala ku Sodom amakhala moyo olekana ndi mulungu ndipo anachita zonyansa zambiri. Mapeto ake mulungu analengeza chiweruzo pa onse kumeneko. Koma zomwe zinachitikira Loti zikuonetsera momwe sitepe imodzi yolekana ndi mulungu ingabweretsere mavuto. Tikuona moyo wa Loti ukumalizidwa ndi chisoni. Ana ake aakazi agona naye malo amodzi pofuna kukonza vuto lomwe amaganizira kuti mulungu analinalo. Izi ndi zotsatira zakusachita zomwe mulungu
    anawalamulira kuti achite. Chenjezo kwa ife lero, mwina tikuyenda ndi ambuye koma pali zinthu zina zomwe tikhumbira molekana ndi mulungu. Tidziwe kunena kuti mathero ake ndi mazunzo chifukwa moyo olekana ndi mulungu umabweretsa
    mavuto azaoneni. Mapeto ake ngati timalingirira kuchita motero, tileke. Moyo olekana ndi mulungu umabweretsa mavuto okhaokha.


     

    Genesis 19:30-38 is ending the story of Sodom and Gomora. The Bible has always honestly told us about human history (it includes

    their short falls and how those contributed to their problems and suffering). In this passage, we find a very valuable lesson; life apart from God only equals suffering. The people of Sodom lived their lives apart from God and did all kinds of bad things and so God declared judgement upon these two cities. But what happens to Lot after this reveals to us just how a small step away from
    God can lead us far away from him and bring problems. We see the life of Lot ending in a pitiful way. His daughters sleep with him in trying to fix what they thought was a problem to God. This is the result of not doing what God told them to do. A warning to each of us, maybe we are walking with the lord today but they are things that we desire apart from God. We should know that one step away from God will equal sorrows for us. And as a result, without God we plan foolish things for ourselves and without God our lives are sad and broken. If you are trying to live your life apart from God, you better stop it today because it is down the drain from there and you will never find peace. This is like that because life apart from God equals suffering.

    37 min
  • Mtima wa munthu/A human heart

    Mateyu 5:8 ikutithandizira kumvetsetsa lingaliro la malo

    opangira katundu. Malo opangira katundu ndi komwe tingapezeko akupanga katundu. Ophunzitsa baibulo odziwika wina ananena kuti, mtima wa munthu ndi malo opangira katundu. Koma katundu wake ndi wotani? Mtima wa munthu ndi malo opangira mafano. Mtima wa munthu nthawi zonse umapanga zinthu za tsopano ndi
    kumapembeza zoterozo. Koma baibulo limanena kuti munthu ndi wa padera, mulungu analenga munthu muchifanizo chake. Cholinga chakuti munthu adzilamulira zinthu pansi paulamulilo wa mulungu. Komanso adzimupembeza. Koma m’malo mwake munthu akusankha kupembeza mafano. Buku la Mateyu 5:8 tikulimbikitsidwa kuti tilolere mulungu kutipatsa mtima ofuna kupembeza mulungu. Ndipo akutilonjeza kuti iye ndiwopezekeratu. Tsopano tidziwe kuti mawu a mulungu ndi mawu a munthu ndi osiyana. Munthu amalephera kukwaniritsa zomwe alonjeza chifukwa alibe kuthekera. Koma
    mulungu akalonjeza kwa iye zili chimozimozi kuti zachitika kale, ndi chifukwa tiyenera kumudalira.  

    Matthew 5:8 helps us to understand the concept of a

    factory. A factory is a place where goods are produced. One famous bible scholar said that a human heart is a factory. Now, what is it that the human heart is producing? In simple terms a human heart is a factory for idols. A human heart is constantly making new things to worship. But the bible tells us that humans
    are unique, we were created in the image of God, to Reflect his authority and to be in a relationship with him which is described as worship. But as a result, our corrupted hearts always want to worship idols. We have traded worshiping the one true God to worshiping idols. But the book of Matthew 5:8 is encouraging us
    to pursue God and promises that we’ll find him and one day we’ll see him in his full glory. Now, the word of God is not like the words of a human being. A human being can make a promise but later on fail to fulfill the promise due to circumstances.
    But that is not the same with God. When God has promised something, it is as good as done. So, we can trust that he will keep his promises.

    48 min
  • Mulungu apulumutsa Loti/God rescues Lot

    Genesis 19:15-29, mu ndime yamalembayi tikupezamo zinthu zingapo zokhuza mulungu. Mulungu ndi wolungama ndi wangwiro, sadzalora tchimo lipite osalangidwa. Tikuona mulungu akuchita ntchito yake yopereka chiweruzo pamene akuononga Sodom ndi Gomora. Koma potengera poyamba paja, taona

    Abrahamu akukambirana ndi mulungu kumupempha kuti asawononge mdzukulu wake Loti. Mulungu akusunga pempho la Abrahamu ndipo akupulumutsa Loti. Izi zikutengera kukhalidwe lina la mulungu, ndipo ndilakuti mulungu ndi wachifundo. Ndipo taona kale akupulumutsa Loti ndi banja lake kuchiweruzo. Kodi kudziwa izi kutanthauzanji kwa Akhristu lero? Tiyenera kukhala opanda chikayiko mwa mulungu. Ngakhale mavuto abwera mulungu adzatipulumutsa ife. Tiyeneranso kupempherera ena mu mpingo ngakhale omwe ali ku mayiko akutali.   

     

    Genesis 19:15-29, in this passage we see several things about God. The first thing is, God is just and righteous and he will not

    let sin go unpunished. We see God exercising his just acts when he destroys Sodom and Gomora. But as seen earlier, Abraham enters a conversation with God asking him to spare his nephew Lot in the judgement. God spares Lot and his family in the judgement. This takes us to another attribute of God which is God is gracious, and we see him keep his promise to spare lot and his family. How does knowing this help Christians today? Well, Christians can rest assured when going through bad conditions and can be confident that God will take care of them just fine.
    It is the responsibility therefore, of each and every Christian to pray for other Christians in the church and in other parts of the world.

    59 min
  • kukhala ndi njala yofuna chilungamo /Growing thirsty for righteousness

    Mateyu 5:6, funso lomveka bwino nali, kodi mumamva ludzu

    ndi chani? Mukapeza chomwe chapangitsa inu kumva ludzu, ludzulo limatha? Buku la Mateyu 5 ndime ya 6, tikuudzidwa za ludzu lofuna Khristu. Ludzu lofuna chilungamo. Kodi mukumasaka kuti mukhutitsidwe ndi chilungamo? Popeza Yesu akunena kuti, odala ndi omwe amva ludzu la chilungamo popeza adzakhutitsidwa. M’mipingo mwathu tikuyenera kukhala anthu omva ludzu la chilungamo chifukwa ambuye wathu Yesu akukulonjeza kuti tidzakhutitsidwa.

     

    Matthew 5:6, here is a simple question, what makes you

    thirsty? And after getting what you thirsted for, are you ever quenched of the thirst? In book of Matthew 5 verse 6, we’re told of the thirst for Christ. The thirst for righteousness? Are you seeking to be filled with righteousness? For Jesus says “happy are those thirsting and hungering for righteousness for they will be filled.” In our churches we should be thirsting and hungering for righteousness and Jesus tells us that we will be filled.    

    34 min

About Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

From the publisher's feed

Sermons and teaching in Chichewa and English

More shows like Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Gospel Life | Malawi, Missions, and More by Josh Hutchens & Isaac Dzimbiri | Gospel Life

Gospel Life | Malawi, Missions, and More

12 Listeners