Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Download on the App Store

Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine episodes

  • Ana A Mulungu/The Children Of God

    1 Yohane 2:28-3:1-10, mawu a mulungu awa akuthandiza onse omwe ndi ake mulungu kuzindikira kuti pamene ife tagulidwa ndi mwazi wake wa Yesu khristu ndife tsopano ana a mulungu. Ana a mulungu amachita chilungamo ndipo ndiwolungama. Onse omwe alimwa khristu amafanana naye iye. Koma ngati pakati pathu pali ena omwe sachita chilungamo ngakhalenso sakonda m'bale wawo, amenewo siake a mulungu koma a mdierekezi.



    1 John 2:28-3:1-10, these words of God are helping us all, children of God to realise that when we were bought by the blood of Christ Jesus, we became his. And now we are known as children of God. The children of God are evident by this fact that whoever does practice righteousness and is just belongs to God. But if one does not, even to love his brother becomes a problem for him then he is of the Devil.   

    48 min
  • Khalani mwa Khristu/Remain in Christ

    1 Yohane 2:18-27, nthawi zambiri anthu amafunsa kuti kodi 'tili nthawi ya masiku omaliza?' Yankho ndi eya. Nthawi ya masiku omaliza ndi pakati pa kubwera kwa Yesu Khristu koyamba ndi kubwera kwa Yesu Khristu kachiwiri. Bukuli likubweretsa poyera nkhani imene ndiyovuta kuyimvetsa. Kodi okana Khristu abwera liti? Paulo akunena motere pakhaniyi, okana Khristu wamkulu adzabwera koma chidwichathu chikhale apa, okana khristu ambiri afika kale. Ndipo ambiri alipakati pathu, mipingo mwadzadza ndi anthu oterewa. Funso nati, kodi ife tili mwa Khristu, kapena gawo lathu ndi lokana Khristu?


    1 John 2:18-27, many times people ask in wonder, are we in the ladder days? The answer is yes. The time between the first coming of Jesus Christ an his second coming marks the end of times or the ladder days. This book brings to light about the most confusing story about the anti christ. About the anti christ, When is the anti christ coming? Paul tells us clear that the great anti christ is coming but our focus should be at the anti christ who are already here. many of them are among us, and in our midst they are rejecting christ. But the question still remains, are we remaining in christ or are we partaking the anti christ?   

    39 min
  • Kondani Mulungu/Love God

    1 Yohane 2:12-17,chifukwa chachikondi chimene tilinacho pa mulungu wathu, timamumvera ndi kutsatira malamulo ake. Choncho timawonetsera ku dziko lonse kuti ndife ake kudzera muchikondi chomwe tilinacho pa mulungu wathu. Ndichifukwa chake abale tiyeni tipitirize monga okhulupirira komanso okonda mulungu ndi kukana dziko lapansi.


    1 John 2:12-17, because of the love we have for God, we continue to love him more. Through our faith, we continue to also obey his commandments. We continue to show the world that we belong to God and that we love him through our living as christians. It is also the reason why brothers, we should continue to love God and continue living as christians and denying the offers of the world.

    57 min
  • Kumvera Mulungu ndi Malamulo ake/Obedient to God and his commandment

    1 Yohane 2:3-11, Buku la 1 Yohane likupitiriza kubwera poyera njira zomwe khristu opulumutsidwa akuyenera kupitiriza kuyenda pa nthawi imene khristu wapulumutsidwa. Kumvera mulungu ndi malamulo ake ndi chiwonetsero chachikulu ndi chilungamo chathu kwa anthu kuti ife timankonda mulungu, timakhulupirira mulungu wathu, zonse zimene mulungu atilamulira kuti tichite ife timamvera ndikuchita.


    1 John 2:3-11, the book of 1 John continues to shade light on principles that true christians are continuously to show in the congregation and to the people who are not part of the church and are regarded as non believers. Obedient to God and his principles shows a sign and our justice to others that we love God and that we obey his principles and all that God commands us we willingly do.       

    59 min
  • Kuyenda mu kuwunika(khalidwe loyamba)/Walking in the light(the first attribute)

    1 Yohane 1:5-2:2, kutchulidwa kuti nkhristu sikungapangise munthu kukhala ndi zimene nkhristu ali nazo. Bukuli muli njira zomwe akhristu akuyenera kuyenda pa chikhristu chawo. Chiyambi cha bukuli tikupeza chiphunzitso cha moyo. Akhristu amene alandira moyo ndipo ali ndi moyo tsopano akuyenera kuyenda mu kuwunika chifukwa ali pa chiyanjano ndi mulungu amene ndi kuwunika.


    1 John 1:5-2:2, to be called a christian cannot make one get all the things a christian has. In this book, many ways are listed for christians to follow when walking in their christianity. The beginning of this book, we read about life. Christians who have received life and now they have life are suppose to walk in the light because they have  fellowship with God who is light.  

    59 min
  • Makhalidwe a chiyanjano mu mpingo/attributes of fellowship in the church

    1 Yohane 1:1-4, moyo weniweni umachokera kwa mulungu ndipo ndi moyo wosatha. Kodi ife tili ndi moyo wosatha? Mulungu amapereka moyo wosatha, ndiye  Yesu Khristu. Uthenga wabwino umabweretsa chiyanjano pakati pa akhristu mu mpingo. Ngati tili ndi moyo wosatha, tidzakhala pa chiyanjano ndi atate ndi mwana ndi mzimu woyera ndi wina ndi zake. Tikuyenera kukhala ndi chiyanjano chimene ndi moyo wosatha.


    1 John 1:1-4, the real life we spoke about, really comes from God and its everlasting life. But do we have everlasting life? God gives his sheep everlasting life and that everlasting life is Jesus Christ. The good news brings about fellowship among christians in the church. If christians have everlasting life, it is evident that they have fellowship with the father, the son, and the Holy Spirit and with their fellow christians. 

    1 hr 1 min
  • Za mkati mwa buku la 1 Yohane/Inside the book of 1 John

    1 Yohane, buku limeneli likupezeka ndi uthenga opasa moyo. Nkhani zomwe zikupezeka mu bukuli kwambiri ndi ndondomeko za kayendedwe ka khristu kuti ndi ziti zomwe akuyenera kuchita khristu komanso ndi ziti zomwe sakuyenera kuchita pamene iye wa pulumutsidwa kapena pamene iye watchulidwa kuti ndi khristu. Khristu aliyense amakhala khristu pamene wabatizidwa ndipo pamene mzimu woyera ali mwa iye. Ndondomeko yomwe ili mu bukuli ikuthandizira akhristu kuzindikira kuti tsopano ndife akhristu pamene mzimu woyera ali mwa ife. 


    1 John, this book contains the word of life. This book is mainly about the way of life of christians. It comprises of what christians are suppose to do and are not suppose to do when are saved and have now received the Holy Spirit and are announced as christians. Every person becomes a christian when have been baptised and have received the Holy Spirit because nobody is born that way. So this book it's all about how can a christian recognise the power of the Holy Spirit operating in him or her and one is able to bare good fruits.

    1 hr 5 min
  • Mtima ngati wa Khristu Yesu/A heart like that of Christ Jesus

    Aphilipi 2:5-8, ma vesi amenewa akulimbikitsa akhristu onse kukhala odzichepetsa monga Yesu Khristu anali odzichepetsa. Yesu anavomera kusiya ulemerero wake ku dziko la kumwamba ndi kubadwira ku banja losauka, kubadwira anthu osauka ndi cholinga choti apeleke chipulumutso ku dziko lonse lapansi ndi kupulumutsa anthu onse ochimwa. Chifukwa cha kudzichepetsa kwa Khristu Yesu lero anthu tonse tili ndi kuthekera kokhala moyo wa chiyembekezo ndikulindilira moyo wosatha. Choncho kubadwa kwa Yesu Khristu kukuyenera kusintha machitidwe athu ndi anthu ena. Yesu akulimbikitsa ubale wolimba pakati pa akhristu omwe ndi mboni za iye.


    Philippians 2:5-8, these verses are encouraging christians to be humble like Jesus Christ was humble. Jesus was humble that he left his glorious home and was born to a poor family and born for poor people so that through that he gives a propitiatory sacrifice for all sinful people and become the salvation for all people. Because of his humbleness, today we have life and hope for the everlasting life to come. In that way, the birth of Jesus Christ should cause christians to have the right attitude towards others. Jesus is encouraging strong brotherhood among fellow christians as we are being his witnesses.

    58 min
  • Chisangalaro choonadi pa kubadwa kwa Yesu Khristu/The real happiness upon the birth of Jesus Christ

    Mateyu 2:1-15, kubadwa kwa ambuye Yesu m'mitima mwathu ndi chinthu chonyaditsa kwambiri. Ndipo chisangalaro chake ndichamtengo wapatali. Anzeru akum'mawa anakondwera kwambiri poona mfumu yobadwayo. Kodi nankha ife lero tikamulandira Yesu Khristu ndikukhala ambuye ndi mpulumutsi wathu timakondwerera motani?


    Matthew 2:1-15, The birth of our lord Jesus in our hearts its a priceless gift. And the happiness that comes with it is also priceless. Wise men from the east upon seeing the king, Jesus Christ they did obeisance to him. And they were really happy after seeing him. What about us today, when we receive christ and acknowledge him as our lord and saviour, how do we celebrate?

    54 min
  • Yesu Khristu ndi uthenga wabwino/Jesus Christ is the good news

    Luka 2:1-14, kubadwa kwa yesu Khristu kunabweretsa chimwemwe pakati pa anthu makamaka okhawo omwe anamudwiwa iye. Ndipo chimwemwe chotere chimapitirira kupezeka pakati pathu. Makamaka mwa ife tonse okhulupirira ndi opulumutsidwa chifukwa timadziwa bwino lomwe kuti Yesu Khristu ndi chifukwa chokhacho tili ndi moyo komanso ndi chiyembekezo.


    Luke 2:1-14, the birth of Jesus Christ brought happiness amongst those who knew him. And that happiness still lives in us believers today. We well know that Jesus is our lord and saviour. And it's because of him that we now have hope.

    49 min

About Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

From the publisher's feed

Sermons and teaching in Chichewa and English

More shows like Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Gospel Life | Malawi, Missions, and More by Josh Hutchens & Isaac Dzimbiri | Gospel Life

Gospel Life | Malawi, Missions, and More

12 Listeners