
Sign up to save your podcasts
Or


Aefeso 4:1-6, Paulo mtumwi akulimbikitsa a khristu kukhala ndi makhalidwe oyenera mayitanidwe awo. Akhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa, oleza mtima, ololerana wina ndi mzake. Akhristuwa achite zonsezi moyetsetsa kusunga umodzi wa mzimu umene umatimangilira pamodzi ndi mtendere.
Ephesians 4:1-6, the apostle Paul is appealing to the christians to walk worthily of the calling with which they were called. With all humility and mildness with patience, putting up with one another in love. Earnestly endeavouring to maintain the oneness of the spirit in the uniting bond of peace.
Afilipi 2:1-4, mundime yamalemba imeneyi Paulo akuthokoza, akulangiza, akulimbikitsa ndi kudzuzura mpingo omwe iye anawuyambitsa ponena kuti "monga mpingo ndi thupi la Khristu Yesu, ziwalo zake kukhala akhristu sakuyenera kukhala ndi migawano, popeza sitingathe kugawa thupi la Khristu Yesu." Motero akulimbikitsa akhristu kukhala ozichepetsa mu mpingo.
Philippians 2:1-4, in this passage Paul is extending his gratitude, encouragement, advice and his rebuke to the church he started by saying "as the church is the body of Christ Jesus, its members being the Christians are not suppose to have divisions in the church, just as we cannot divide the body of Christ Jesus." So he is encouraging christians to have humility in the church.
Genesis 11:10-32, mibado yonse kuyambira pa Adamu, Seti, Nowa, Semu komanso abramu yemwe anasinthidwa kukhala Abrahamu ikutitengera kwa Yesu Khristu yemwe ndi chipulumutso cha anthu onse. Ife tonse ndiodala kamba koti tilimunthawi yomwe milodzo inafika kumathero ndipo chipulumutso chinapelekedwa. Ife tingoyenera kukhulupirira Yesu kukhala mpulumutsi ndi ambuye ndipo tipulumutsidwa.
Genesis 11:10-32, all the generations starting with Adam, Seth, Noah, Shem and Abram who later became Abraham, all are leading us to Jesus Christ who is the salvation of all people. All of us today are blessed because we're in the time where all the signs leading us to Jesus came to an end and the salvation was given. All we need to do is to believe that Jesus is our lord and saviour and we are going to be saved.
Genesis 11:1-9, nthawi zambiri timakamba zokhuza umodzi mokondwera mkumati umodzi ndi mphamvu. Kodi ndi chonchodi? Eya, mokuti Baibulo limalimbikitsa umodzi kufikira pakuti Yesu anati, pali awiri nanenso ndimakhala pomwepo. Koma umodzi omwe ulinga wa Nimurodi, ziwani kuti mulungu amadana nawo ndipo amatsika kuzadzetsa kusamvana pakati pa onse ozondosa zabwino kusandusa zoipa.
Genesis 11:1-9, most of the times we speak of oneness with joy saying, in oneness there is power. But is that true? Yes it is, the Bible encourages oneness to the point that Jesus said, where they're two people am also there. But the oneness that mimic Nimrod, better know that God hates that and he comes down and cause confusion amongst those who exchanges goodness for badness.
Genesis 10:1-32, mu chaputara chimenechi tikuona ndandanda wa ana a Nowa. Koma nkhani yayikulu yagona pa Semu. Kuchokera kwa Semu kunabadwa mwana yemwe anabereka mwana yemwe anaberekanso mwana yemwe anali tate wa Abrahamu komwe mbewu ya mzimayi ikudzera kufikira pa Yesu Khristu. Mulungu atalonjeza kwa mzimayi uja mumachaputara oyambirira aja za mbewu yomwe izaphwanya mutu wanjoka mubukuli, tikuona kuti akusunga pangano lake pomwe akusunga mbewu imeneyi kudzera mwa Semu. Mulungu amakwaniritsa malonjezano ake.
Genesis 10:1-32, in this chapter we are getting the full detailed genealogy of the sons of Noah and their descendants. But the main story focuses on Shem. It is from Shem where a son was born who gave birth to a son who later on became the father of Abraham through whom the seed of a woman continued until Jesus Christ. After God promised the seed of a woman in the early chapters of this book, God preserves that seed through Shem until Abraham and so on and so forth. God fulfils his promises.
Genesis 9:18-28, Nowa atatuluka mchombo anayamba kulima nthaka monga momwe Adamu ankachitira. Nowa anali munthu woyambilira kulima mphesa. Munkhaniyonse tikuona kuti kumapeto kwake kwa kulima mphesaku kukubweretsa mavuto omwe anatsatiridwa ndi themberero. Tikuonanso kuti ana aamuna a Nowa ndikomwe kunachokera mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi. Zimene nkhaniyi ikutanthauza ndi izi: nthawi zonse makolo amakhala ndi udindo wawukulu ophunzitsa anawo njira zoti ayendemo ndipo anawo zomwe aphunzitsidwa ndi zomwezo azakhale kutsogolo. Nde nchifukwa chake makolo ngati saphunzitsa ana awo makhalidwe abwino, anawo azalangidwa. Komanso sibwino kumafunira ena zoipa, m'malo mwake kumawapempherera popeza tonsefe ndife amodzi mwa khristu yesu.
Genesis 9:18-28, After Noah came out of the ark, he started cultivating the land just like Adam did. Noah was the first to cultivate the vine yard. Then the whole story tells us that the cultivating of the vine yard ends with problems followed by a curse. We also see that the world's population came from the three sons of Noah. What the story means: all the time parents have the big responsibility of teaching their children the right way they should go. And whatever the children are taught, that will be conducted through out their whole lives. Then that's why, if parents do not teach their children the righteous way and they are wicked they will nee punished. And also, its not good to wish ill upon others, instead pray for them/each other for we are one in christ Jesus.
Genesis 9:8-17, Mulungu atakondweretsedwa ndi Nowa chifukwa cha kumvera kwake, anamudalitsa namuuza kuti "abelekane ndipo adzadze dziko lapansi ndikuligonjetsa." kenaka Mulungu anachita naye pangano Nowa namuuza kuti sazawononganso dziko lapansi ndi madzi. Izi zinali zosangalasa kwa Nowa ndi banja lake. Komatu izi sizikutanthauza kuti Mulungu sazalanganso dziko lapansi chifukwa cha machimo a anthu. Ayi konse, zowona zake n'zakuti, kuli chilango china chomwe chasungilidwa anthu ochimwa chomwe ndi chowopsa kuposa chanthawi ya Nowa.
Genesis 9:8-17, After God was pleased with Noah because of his obedience, he blessed him and told him to "be fruitful and become many and subdue the earth." Then God went on and made a covenant with Noah. He said 'never again will I destroy the earth with flooding waters.' This was good news for Noah and his family. But does that mean that God will never destroy wicked people? Not at all, in fact the bible says that there is a greater judgement restored for those who are wicked and disobedient to God and it is severe than that of Noah.
Genesis 9:1-7, Noah did everything that God asked of him, he never questioned God or refuse his commandments. But followed God's instructions through out his entire life even when building the Ark, he kept on following God's own directions. And because of this, God was impressed with Noah, so he blessed him and told him that "be fruitful and multiply, fill the earth and subdue it." This is like wise to us christians today, if we obey God's word and follow his instructions, it is to no doubt that he will bless us like he did Noah.
Genesis 9:1-7, Nowa anachita zonse zomwe Mulungu anamulamulira, iye sanafunse konse zochita za Mulungu kapena kukana malaturo ake. Koma anatsatira malangizo a Mulungu moyo wake wonse ingakhale pomanga chombo, anapitilira kutsatirarabe malangizo ake. Ndipo chifukwa cha ichi, Mulungu anakondwera naye Nowa namudalitsa kuti mubelekane ndi kuchulukana ndi kuligonjetsa dziko la pansi. Izi zili chimozimozi ifenso a khristu lero, ngati timvera mulungu ndi mawu ake, popanda kukayikira Mulungu adzatidalitsa nafenso monga momwe anachitira Nowa.
Revelation chapter 8, Dr Eric continues exploring the book of revelation. The book of revelation, for proper understanding of the book, two things to consider; 1) the use of metaphoric language. this is important to take note of, because it would be very difficult to take everything you hear in the book to be literal. for example, when the book talks about the beast of ten horns and the face of a lion, that is metaphoric it's not literal. 2) the book of revelation is written in a loop, meaning to say its sayings and meanings are constructed in a way that is considered to be known as a loop not linear structuring, thus if you happen to read the book as you would any other books, having the beginning, body then the end, you would miss out everything. In this chapter, we hear of the seven trumpets. These are the judgements God is pouring out on the earth. The judgements goes along, chapters 9, 10, 11 up to 13. And the of exodus helps us to understand more of these judgements by shading the picture of how they are to take place. In chapter 7 of exodus, God frees his people with his majestic hand by using the ten plagues. The same, God will do to free his people once and for all with his hand by the means of the judgements also known as the seven trumpets.
Chivumbulutso 8, Dr Eric akupitiliza kuwunikira zomwe zikuchitika mu buku la chivumbuliutso. Buku la chivumbulutso, kuti munthu ukhale ndi kumvetsesa koyenerera kwa bukuli, njira ziwiri zikuyenera kusatidwa. 1) kagwiritsidwe ntchito ka mizembayiso. bukuli likamakamba za Chilombo cha nyá'nga khumi limodzi ndi khope ya nkango, ndizembayiso umenewo. Kuzilingalira malinga ndi mmowe zikumvekera ndekuti uthenga onse usokonezeka kamvekedwe kake. 2) buku la chivumbulutso linalembedwa mozungulira, mokuti munthu ngati angawerenge bukuli monga achitira mabuku ena omwe amakhala ndi chiyambi kenaka thunthu kumaliza ndi chimaliziro ndekuti uthenga onse waphonyedwa. Mu chaputara cha 8, tkuwuzidwa za malipenga asanu ndi awiri, omwe akuyimirira chiweruzo cha mulungu pa dziko lapansi. Chiweruzochi chikuyenda mu machaputara awa 9, 10, 11 mpaka 13. Komanso buku la exodo 7, limathandiziranso kumvetsesa kowonjezera makamaka momwe chiweruzo chomwe chili mbuku la chivumbulutso chikuchitikira.
Chivumbulutso chaputara 7, mu chaputara chimenechi Dr. Eric akupitiliza kubweletsa poyera za nsautso waukulu m'masiku omaliza. Kamvetsetsedwe ka nthawiyi kakupitilirabe kukhala kovutirapo kwa anthu ena kamba kuti kalembedwe kozembayisa kakupitilirabe kupezeka ingakhale mu chaputarachi. Panthawi yomweyo tikuona kuti Paulo akulemba chaputarachi mundondomeko yomwe ingafananizilidwe ndi mapiri omwe patali akuoneka ngati Phiri limodzi koma pomwe uwandikira ndipomwe ungazindikire kuti ndi mapiri omwe akupezeka mondondozana. Zinthu zochitika m'masiku omalizawa zikupezeka zomwe zikutchulidwa kuti zimatiro zisanu ndi ziwiri zomwenso kalembedwe kake ndi kozembayisa. Munthawi imeneyi ndichanzeru kuzifunsa kuti kodi tili mbali iti? popeza nthawi nde yatha kale.
Revelation chapter 7, in this chapter Dr. Eric continues to explore the great tribulation in the ladder days. The understanding of the ladder days and the great tribulation continues to be hard to others as the chapter continues to have the writings that uses the metaphoric language. And at the very time, we see that Paul is writing the chapter in a loop which also can be liken to mountains, from afar, they look like one big mountain but as you get closer and closer, you begin to see that they are but many mountains as you move along them. The great tribulation is also told in the way that the seven scrolls unfolds. At this point it is right to ask the question what side are you on? as we see the days drawing near to the end.
From the publisher's feed

12 Listeners